Amenewo ndiwo mau walamulira Yehova, Aoleko yense monga mwa njala yake; munthu mmodzi omeri limodzi, monga momwe muli, yense atengere iwo m'hema mwake.
Eksodo 16:22 - Buku Lopatulika Ndipo kunali tsiku lachisanu ndi chimodzi, anaola mkate, naonjezapo linzake, maomeri awiri pa munthu mmodzi; ndipo akazembe a khamulo anadza nauza Mose. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunali tsiku lachisanu ndi chimodzi, anaola mkate, naonjezapo linzake, maomeri awiri pa munthu mmodzi; ndipo akazembe a khamulo anadza nauza Mose. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi ankatola chakudya cha masiku aŵiri, chokwanira malita anai ndi theka pa munthu mmodzi. Ndipo atsogoleri onse a Aisraele adabwera kwa Mose kudzamuuza zimenezo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsiku lachisanu ndi chimodzi anatuta malita anayi munthu aliyense, ndipo atsogoleri a mpingo wonse anabwera kudzawuza Mose za zimenezi. |
Amenewo ndiwo mau walamulira Yehova, Aoleko yense monga mwa njala yake; munthu mmodzi omeri limodzi, monga momwe muli, yense atengere iwo m'hema mwake.
Ndipo anauola m'mawa ndi m'mawa, yense monga mwa njala yake; popeza likatentha dzuwa umasungunuka.
Ndipo kudzakhala tsiku lachisanu ndi chimodzi, kuti azikonza umene adabwera nao, ataonjezapo muyeso unzake wa pa tsiku limodzi.
Koma Mose anawaitana; ndipo Aroni ndi akazembe onse a khamu la anthu anabwera kwa iye; ndipo Mose analankhula nao.
Popeza ndicho chaka choliza lipenga; muchiyese chopatulika, mudye zipatso zake kunja kwa munda.
Ndipo mubzale chaka chachisanu ndi chitatu, ndi kudya zipatso zasundwe; kufikira chaka chachisanu ndi chinai, mpaka zitacha zipatso zake mudzadya zasundwe.