Eksodo 14:7 - Buku Lopatulika napita nao magaleta osankhika mazana asanu ndi limodzi, ndi magaleta onse a mu Ejipito, ndi akapitao ao onse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 napita nao magaleta osankhika mazana asanu ndi limodzi, ndi magaleta onse a m'Ejipito, ndi akapitao ao onse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adatenga magaleta amphamvu 600 pamodzi ndi magaleta ena onse ndipo adaika atsogoleri pa magaleta onsewo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anatenga magaleta 600 abwino kwambiri pamodzi ndi magaleta ena a dziko la Igupto. Anatenganso akuluakulu onse ankhondo. |
Ena atama magaleta, ndi ena akavalo; koma ife tidzatchula dzina la Yehova Mulungu wathu.
Magaleta a Mulungu ndiwo zikwi makumi awiri, inde zikwi zowirikizawirikiza, Ambuye ali pakati pao, monga mu Sinai, m'malo opatulika.
Ndipo Aejipito anawalondola, nalowa pakati pa nyanja powatsata, ndiwo akavalo onse a Farao, magaleta ake, ndi apakavalo ake.
Ndipo Yehova analimbitsa mtima wa Farao, mfumu ya Aejipito, ndipo iye analondola ana a Israele; koma ana a Israele adatuluka ndi dzanja lokwezeka.
Magaleta a Farao ndi nkhondo yake anawaponya m'nyanja; ndi akazembe ake osankhika anamira mu Nyanja Yofiira.
Wamtonza Ambuye ndi atumiki ako, ndipo wati, Ndi khamu la magaleta anga ine ndafika kunsonga za mapiri, kumbali za Lebanoni; ndipo ndidzagwetsapo mikungudza yaitali, ndi milombwa yosankhika; ndipo ine ndidzafika pamutu pake penipeni, kunkhalango ya munda wake wobalitsa.
Ndipo Yehova anaononga Sisera ndi magaleta onse ndi gulu lankhondo lonse, ndi lupanga lakuthwa pamaso pa Baraki; koma Sisera anatsika pagaleta nathawa choyenda pansi.
Ndipo ana a Israele anafuula kwa Yehova; pakuti anali nao magaleta achitsulo mazana asanu ndi anai; napsinja ana a Israele kolimba zaka makumi awiri.