Munawatsogoleranso usana ndi mtambo woti njo, ndi moto tolo usiku, kuwaunikira m'njira akayendamo.
Eksodo 13:22 - Buku Lopatulika sanachotse mtambo usana, kapena mtambo wamoto usiku, pamaso pa anthu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 sanachotse mtambo usana, kapena mtambo wamoto usiku, pamaso pa anthu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthaŵi zonse chipilala chamtambo chinkatsogolera anthu masana, ndipo chipilala chamoto chinkaŵatsogolera usiku. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Usana, chipilala cha mtambo ndi usiku, chipilala cha moto zinali patsogolo kuwatsogolera anthu aja. |
Munawatsogoleranso usana ndi mtambo woti njo, ndi moto tolo usiku, kuwaunikira m'njira akayendamo.
koma Inu mwa nsoni zanu zazikulu simunawasiye m'chipululu; mtambo woti njo sunawachokere usana kuwatsogolera m'njira, ngakhale moto wa tolo usiku kuwaunikira panjira anayenera kuyendamo.
Ndipo mthenga wa Mulungu, wakutsogolera ulendo wa Israele, unachokako, nutsata pambuyo pao; ndipo mtambo njo uja unachoka patsogolo pao, nuima pambuyo pao;
Pakuti mtambo wa Yehova unakhala pa chihema msana, ndi usiku munali moto m'menemo, pamaso pa mbumba yonse ya Israele, m'maulendo ao onse.
Ndipo Yehova adzalenga pokhala ponse paphiri la Ziyoni, ndi pa misonkhano yake, mtambo ndi utsi usana, ndi kung'azimira kwa malawi a moto usiku; chifukwa kuti pa ulemerero wonse padzayalidwa chophimba.
Ndipo tsiku loutsa Kachisi mtambo unaphimba Kachisi, ndiwo chihema chokomanako; ndicho chihema chaumboni, ndipo madzulo padaoneka pa Kachisi ngati moto, kufikira m'mawa.
Ndipo ndinaona mngelo wina wolimba alikutsika Kumwamba, wovala mtambo; ndi utawaleza pamutu pake, ndi nkhope yake ngati dzuwa, ndi mapazi ake ngati mizati yamoto;