Eksodo 13:21 - Buku Lopatulika21 Ndipo Yehova anawatsogolera usana ndi mtambo njo kuwatsogolera m'njira; ndi usiku ndi moto njo, wakuwawalitsira; kuti ayende usana ndi usiku; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201421 Ndipo Yehova anawatsogolera usana ndi mtambo njo kuwatsogolera m'njira; ndi usiku ndi moto njo, wakuwawalitsira; kuti ayende usana ndi usiku; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa21 Nthaŵi yamasana Chauta ankaŵatsogolera ndi chipilala chamtambo namaŵalangiza njira. Ndipo nthaŵi yausiku, ankaŵatsogolera ndi chipilala chamoto, kuŵaunikira njira kuti aziyenda masana ndi usiku womwe. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero21 Nthawi yamasana Yehova amakhala patsogolo pa anthu kuwatsogolera njira ndi chipilala cha mtambo, ndipo usiku Yehova ankawatsogolera ndi chipilala cha moto, kuwawunikira njira kuti athe kuyenda masana ndi usiku. Onani mutuwo |