Pamenepo Mose anaitana akulu onse a Israele, nanena nao, Pitani, dzitengereni anaankhosa monga mwa mabanja anu, nimuphere Paska.
Eksodo 13:13 - Buku Lopatulika Koma woyamba yense wa bulu uzimuombola ndi mwanawankhosa; ndipo ukapanda kumuombola uzimthyola khosi; koma oyamba onse a munthu mwa ana ako uziwaombola. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma woyamba yense wa bulu uzimuombola ndi mwanawankhosa; ndipo ukapanda kumuombola uzimthyola khosi; koma oyamba onse a munthu mwa ana ako uziwaombola. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma mwanawabulu woyamba kubadwa, muzimuwombolanso pakupereka mwanawankhosa m'malo mwake. Ngati simufuna kumuwombola, muzimthyola khosi. Muziwombola mwana wamwamuna wachisamba aliyense. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma mwana woyamba kubadwa wa bulu muzikamuwombola ndi mwana wankhosa, koma ngati simukamuwombola, muzikamuthyola khosi. Mwana wamwamuna woyamba kubadwa muzikamuwombola. |
Pamenepo Mose anaitana akulu onse a Israele, nanena nao, Pitani, dzitengereni anaankhosa monga mwa mabanja anu, nimuphere Paska.
Mulankhule ndi gulu lonse la Israele ndi kuti, Tsiku lakhumi la mwezi uno adzitengere munthu yense mwanawankhosa, monga mwa mabanja a atate ao, mwanawankhosa pabanja.
Ndipatulire Ine yense woyamba kubadwa, wotsegulira pa amake mwa ana a Israele, mwa anthu ndi mwa zoweta; ndiwo anga.
Koma woyamba wa bulu uzimuombola ndi mwanawankhosa; ukapanda kumuombola, uzimthyola khosi. Ana anu aamuna oyamba onse uziwaombola. Ndipo asamaoneka pamaso panga opanda kanthu.
Iwo ndiwo amene sadetsedwa pamodzi ndi akazi; pakuti ali anamwali. Iwo ndiwo amene atsata Mwanawankhosa kulikonse amukako. Iwowa anagulidwa mwa anthu, zipatso zoyamba kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.