Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 13:13 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Koma mwana woyamba kubadwa wa bulu muzikamuwombola ndi mwana wankhosa, koma ngati simukamuwombola, muzikamuthyola khosi. Mwana wamwamuna woyamba kubadwa muzikamuwombola.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

13 Koma woyamba yense wa bulu uzimuombola ndi mwanawankhosa; ndipo ukapanda kumuombola uzimthyola khosi; koma oyamba onse a munthu mwa ana ako uziwaombola.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Koma woyamba yense wa bulu uzimuombola ndi mwanawankhosa; ndipo ukapanda kumuombola uzimthyola khosi; koma oyamba onse a munthu mwa ana ako uziwaombola.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Koma mwanawabulu woyamba kubadwa, muzimuwombolanso pakupereka mwanawankhosa m'malo mwake. Ngati simufuna kumuwombola, muzimthyola khosi. Muziwombola mwana wamwamuna wachisamba aliyense.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 13:13
7 Mawu Ofanana  

Ndipo Mose anasonkhanitsa akuluakulu onse a Israeli nati, “Pitani msanga kukasankha nkhosa zokwanira pa mabanja anu, ndipo muziphe ngati Paska.


Muliwuze khamu lonse la Israeli kuti pa tsiku la khumi la mwezi uno, munthu aliyense asankhire banja lake mwana wankhosa mmodzi. Banja lililonse litenge mwana wankhosa mmodzi.


“Ana onse aamuna oyamba kubadwa uwapatule, ndi anga. Aliyense woyamba kubadwa pakati pa Aisraeli ndi wanga, kaya ndi wa munthu kapena wa chiweto.”


Muziwombola mwana woyamba kubadwa wa bulu popereka mwana wankhosa. Mukapanda kumuwombola mupheni. Muziwombola ana anu onse aamuna. “Palibe ndi mmodzi yemwe adzaonekere pamaso panga wopanda kanthu mʼdzanja lake.


Awa ndiwo amene sanadzidetse koma anadzisunga ndipo sanadziyipitse ndi akazi. Anthu amenewa ndiwo ankatsatira Mwana Wankhosa kulikonse kumene ankapita. Ndiwo amene anagulidwa pakati pa anthu a dziko lapansi kuti akhale oyambirira kuperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwana Wankhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa