Eksodo 34:20 - Buku Lopatulika20 Koma woyamba wa bulu uzimuombola ndi mwanawankhosa; ukapanda kumuombola, uzimthyola khosi. Ana anu aamuna oyamba onse uziwaombola. Ndipo asamaoneka pamaso panga opanda kanthu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201420 Koma woyamba wa bulu uzimuombola ndi mwanawankhosa; ukapanda kumuombola, uzimthyola khosi. Ana anu amuna oyamba onse uziwaombola. Ndipo asamaoneka pamaso panga opanda kanthu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa20 Koma muzidzaombola mwana woyamba kubadwa wa bulu, pakupereka nkhosa m'malo mwake. Mukapanda kumuwombola, muzidzamthyola khosi. Mwana aliyense wachisamba wamwamuna, muzidzachita choombola. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaonekere pamaso panga opanda kanthu kumanja kodzapereka. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero20 Muziwombola mwana woyamba kubadwa wa bulu popereka mwana wankhosa. Mukapanda kumuwombola mupheni. Muziwombola ana anu onse aamuna. “Palibe ndi mmodzi yemwe adzaonekere pamaso panga wopanda kanthu mʼdzanja lake. Onani mutuwo |