Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 12:3 - Buku Lopatulika

3 Mulankhule ndi gulu lonse la Israele ndi kuti, Tsiku lakhumi la mwezi uno adzitengere munthu yense mwanawankhosa, monga mwa mabanja a atate ao, mwanawankhosa pabanja.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Mulankhule ndi msonkhano wonse wa Israele ndi kuti, Tsiku lakhumi la mwezi uno adzitengere munthu yense mwanawankhosa, monga mwa mabanja a atate ao, mwanawankhosa pabanja.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Mulengeze kwa khamu lonse la Aisraele kuti pa tsiku lakhumi la mwezi uno, munthu aliyense adzasankhulire banja lake mwanawankhosa mmodzi. Banja lililonse lidzatenge mwanawankhosa mmodzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Muliwuze khamu lonse la Israeli kuti pa tsiku la khumi la mwezi uno, munthu aliyense asankhire banja lake mwana wankhosa mmodzi. Banja lililonse litenge mwana wankhosa mmodzi.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 12:3
26 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu anati, Mwana wanga, Mulungu adzadzifunira yekha mwanawankhosa wa nsembe yopsereza; nayenda pamodzi onse awiri.


Ndiponso Abele anatenga iyenso mwana woyamba wa nkhosa zake ndi mafuta omwe. Yehova ndipo anayang'anira Abele ndi nsembe yake:


Ndipo Yosiya anapatsa ana a anthu zoweta, anaankhosa ndi a mbuzi zikhale zonsezo za nsembe za Paska kwa aliyense anali komweko; zinafikira zikwi makumi atatu, ndi ng'ombe zikwi zitatu, ndizo zotapa pa chuma cha mfumu.


Mwezi uno uzikhala kwa inu woyamba wa miyezi; muziuyesa mwezi woyamba wa chaka.


Pamenepo Mose anaitana akulu onse a Israele, nanena nao, Pitani, dzitengereni anaankhosa monga mwa mabanja anu, nimuphere Paska.


Banja likaperewera mwanawankhosa, munthu ndi mnzake ali pafupi pa nyumba yake atenge monga mwa kufikira kwa anthu ao; muziwerengera mwanawankhosa monga mwa kudya kwao.


Ndipo mukhale naye chisungire kufikira tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi womwe; ndipo gulu lonse la Israele lizamuphe madzulo.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ufuuliranji kwa Ine? Lankhula ndi ana a Israele kuti aziyenda.


Ndipo anati kwa Mose, Mulankhule nafe ndinu, ndipo tidzamva; koma asalankhule nafe Mulungu, kuti tingafe.


ndipo Aroni anawafotokozera mau onse amene Yehova adauza Mose, nachita zizindikiro zija pamaso pa anthu.


Chifukwa chake nena kwa ana a Israele Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani pansi pa akatundu a Aejipito ndipo ndidzakulanditsani ku ukapolo wanu; ndipo ndidzakuombolani ndi dzanja lotambasuka, ndi maweruzo aakulu;


Chaka cha makumi awiri ndi zisanu cha undende wathu, poyamba chaka, tsiku lakhumi lamwezi, chaka chakhumi ndi zinai atakantha mzindawo, tsiku lomwelo, dzanja la Yehova linandikhalira; ndipo anamuka nane komweko.


Lankhula ndi ana a Israele, nunene nao, Aliyense mwa inu akabwera nacho chopereka cha kwa Yehova, muzibwera nacho chopereka chanu chikhale cha zoweta, cha ng'ombe, kapena cha nkhosa, kapena cha mbuzi.


nadze nayo nsembe yopalamula kwa Yehova chifukwa cha kulakwa kwake adachimwira, ndiyo nkhosa yaikazi, kapena mbuzi yaikazi, ikhale nsembe yauchimo; ndipo wansembe amchitire chomtetezera chifukwa cha kuchimwa kwake.


Kudzatero ndi ng'ombe iliyonse, kapena nkhosa yamphongo iliyonse, kapena mwanawankhosa aliyense, kapena mwanawambuzi aliyense.


M'mawa mwake anaona Yesu alinkudza kwa iye, nanena, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa tchimo lake la dziko lapansi!


ndipo poyang'ana Yesu alikuyenda, anati, Onani Mwanawankhosa wa Mulungu!


Pomwepo anatsala masiku asanu ndi limodzi asanafike Paska, Yesu anadza ku Betaniya kumene kunali Lazaro, amene Yesu adamuukitsa kwa akufa.


M'mawa mwake khamu lalikulu la anthu amene adadza kuchikondwerero, pakumva kuti Yesu alinkudza ku Yerusalemu,


Tsukani chotupitsa chakale, kuti mukakhale mtanda watsopano, monga muli osatupa. Pakutinso Paska wathu waphedwa, ndiye Khristu;


Koma m'mawa adzakuyandikitsani, fuko ndi fuko; ndipo kudzali kuti fukoli Yehova aliwulula lidzayandikira mwa zibale zake; ndi chibale Yehova achiwulula chidzayandikira monga mwa a nyumba ake; ndi a m'nyumbawo Yehova awawulula adzayandikira mmodzimmodzi.


Ndipo adzachilambira onse akukhala padziko, amene dzina lao silinalembedwe m'buku la moyo la Mwanawankhosa, wophedwa kuyambira makhazikidwe a dziko lapansi.


Ndipo Samuele anatenga mwanawankhosa woyamwa, nampereka wathunthu kwa Yehova, nsembe yopsereza; ndipo Samuele anapempherera Israele kwa Yehova; ndipo Yehova anamvomereza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa