Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 12:4 - Buku Lopatulika

4 Banja likaperewera mwanawankhosa, munthu ndi mnzake ali pafupi pa nyumba yake atenge monga mwa kufikira kwa anthu ao; muziwerengera mwanawankhosa monga mwa kudya kwao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Banja likaperewera mwanawankhosa, munthu ndi mnzake ali pafupi pa nyumba yake atenge monga mwa kufikira kwa anthu ao; muziwerengera mwanawankhosa monga mwa kudya kwao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Banja likachepa, kuti silingathe kudya nyama yonseyo, mabanja aŵiri oyandikana aphatikizane pamodzi, monga momwe aliri anthu, tsono onsewo adyere limodzi. Mulinganiziretu chiŵerengero cha anthu odya nyamayo, modziŵa m'mene munthu mmodzi angadyere.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ngati banja lili lochepa moti silingathe kudya nyama yonse ya nkhosa, ligawane ndi banja lomwe layandikana nalo nyumba. Mabanja adziwiretu chiwerengero cha anthu amene alipo pokonzekera zimenezi. Muwerengere kuchuluka kwa nyama imene anthu adzadye potengera mmene munthu mmodzi angadyere.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 12:4
4 Mawu Ofanana  

Lero ndili nazo zaka makumi asanu ndi atatu; kodi ndikhoza kuzindikiranso kusiyanitsa zabwino ndi zoipa? Mnyamata wanu ndikhoza kodi kuzindikira chimene ndidya kapena kumwa? Kodi ndikhozanso kumva mau a amuna ndi akazi oimba? Chifukwa ninji tsono mnyamata wanu ndidzakhalanso wolemetsa mbuye wanga mfumu.


Mulankhule ndi gulu lonse la Israele ndi kuti, Tsiku lakhumi la mwezi uno adzitengere munthu yense mwanawankhosa, monga mwa mabanja a atate ao, mwanawankhosa pabanja.


Mwanawankhosa wanu azikhala wangwiro, wamwamuna, wa chaka chimodzi; muzimtenga ku nkhosa kapena ku mbuzi.


Ndipo ophunzira anachita monga Yesu anawauza, nakonza Paska.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa