Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 12:5 - Buku Lopatulika

5 Mwanawankhosa wanu azikhala wangwiro, wamwamuna, wa chaka chimodzi; muzimtenga ku nkhosa kapena ku mbuzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Mwanawankhosa wanu azikhala wangwiro, wamwamuna, wa chaka chimodzi; muzimtenga ku nkhosa kapena ku mbuzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Mwanawankhosa wake adzakhale wopanda chilema, wamphongo, wa chaka chimodzi. Mungathe kusankhulanso mwanawambuzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ziweto zimene musankhe ziyenera kukhala zazimuna za chaka chimodzi, zopanda chilema, ndipo zikhale nkhosa kapena mbuzi.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 12:5
14 Mawu Ofanana  

Banja likaperewera mwanawankhosa, munthu ndi mnzake ali pafupi pa nyumba yake atenge monga mwa kufikira kwa anthu ao; muziwerengera mwanawankhosa monga mwa kudya kwao.


Ndipo chopereka chake chikakhala cha nkhosa, kapena cha mbuzi, chikhale nsembe yopsereza; azibwera nayo yaimuna yopanda chilema.


Chopereka chake chikakhala nsembe yopsereza ya ng'ombe, azibwera nayo yaimuna yopanda chilema; abwere nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuti alandirike pamaso pa Yehova.


Ndipo tsiku loweyula mtolowo, ukonze mwanawankhosa wopanda chilema, wa chaka chimodzi, akhale nsembe yopsereza ya Yehova.


Koma wotembereredwa wonyengayo, wokhala nayo yaimuna m'gulu lake, nawinda, naphera Yehova nsembe chinthu chachilema; pakuti Ine ndine mfumu yaikulu, ati Yehova wa makamu; ndipo dzina langa ndi loopsa pakati pa amitundu.


ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;


ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;


Musamaphera Yehova Mulungu wanu nsembe ya ng'ombe, kapena nkhosa, yokhala nacho chilema, kapena chilichonse choipa; pakuti chinyansira Yehova Mulungu wanu.


Pakuti mkulu wa ansembe wotere anatiyenera ife, woyera mtima, wopanda choipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa, wakukhala wopitirira miyamba;


Saulo anali ndi zaka makumi atatu pamene anayamba ufumu wake; nakhala mfumu ya Israele zaka ziwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa