Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 12:5 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ziweto zimene musankhe ziyenera kukhala zazimuna za chaka chimodzi, zopanda chilema, ndipo zikhale nkhosa kapena mbuzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

5 Mwanawankhosa wanu azikhala wangwiro, wamwamuna, wa chaka chimodzi; muzimtenga ku nkhosa kapena ku mbuzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Mwanawankhosa wanu azikhala wangwiro, wamwamuna, wa chaka chimodzi; muzimtenga ku nkhosa kapena ku mbuzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Mwanawankhosa wake adzakhale wopanda chilema, wamphongo, wa chaka chimodzi. Mungathe kusankhulanso mwanawambuzi.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 12:5
14 Mawu Ofanana  

Ngati banja lili lochepa moti silingathe kudya nyama yonse ya nkhosa, ligawane ndi banja lomwe layandikana nalo nyumba. Mabanja adziwiretu chiwerengero cha anthu amene alipo pokonzekera zimenezi. Muwerengere kuchuluka kwa nyama imene anthu adzadye potengera mmene munthu mmodzi angadyere.


“ ‘Koma ngati chopereka cha nsembe yopserezayo ndi nkhosa kapena mbuzi kuchokera pa ziweto zake, munthuyo apereke yayimuna yopanda chilema.


“ ‘Ngati munthu apereka nsembe yopsereza ya ngʼombe, ikhale yayimuna yopanda chilema. Aziyipereka pa khomo la tenti ya msonkhano, kuti Yehova alandire.


Pa tsiku limene muweyula mtolowo, muperekenso mwana wankhosa wa mwamuna wa chaka chimodzi, wopanda chilema kuti akhale nsembe yopsereza ya kwa Yehova.


“Atembereredwe munthu wachinyengo amene ali ndi nyama yayimuna yabwino mʼgulu la ziweto zake ndipo analumbira kuyipereka, koma mʼmalo mwake nʼkupereka nsembe kwa Ambuye nyama yosayenera. Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Pakuti ndine mfumu yayikulu, dzina langa liyenera kuopedwa pakati pa anthu a mitundu yonse.’ ”


mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa imodzi ndi mwana wankhosa mmodzi wamwamuna wa chaka chimodzi, za nsembe yopsereza;


mwana wangʼombe wamwamuna mmodzi, nkhosa yayimuna imodzi ndi mwana wankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, nsembe yopsereza;


Musapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wanu ngʼombe kapena nkhosa imene ili ndi chilema kapena cholakwika chilichonse, pakuti zimenezi zimamunyansa.


Uyu ndi Mkulu wa ansembe amene tikumufuna chifukwa ndi woyera, wopanda choyipa kapena chodetsa chilichonse, wosiyana ndi anthu ochimwa, ndiponso wokwezedwa kuposa zonse zakumwambaku.


Sauli analowa ufumu ali ndi zaka makumi atatu, ndipo analamulira Israeli kwa zaka 42.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa