Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 12:48 - Buku Lopatulika

Koma akakhala nanu mlendo, nakonzera Yehova Paska, adulidwe amuna ake onse, ndipo pamenepo asendere kuuchita; nakhale ngati wobadwa m'dziko; koma wosadulidwa aliyense asadyeko.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma akakhala nanu mlendo, nakonzera Yehova Paska, adulidwe amuna ake onse, ndipo pamenepo asendere kuuchita; nakhale ngati wobadwa m'dziko; koma wosadulidwa aliyense asadyeko.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mlendo akakhala pakati panu, namafuna kuti achite nao mwambo wa Paska ya Chauta, muziyamba mwaumbala amuna onse am'banjamo. Pambuyo pake angathe kuloŵa ndi kumachita nao mwambowo. Iyeyo muzimuyesa ngati mbadwa yeniyeni ya Israele. Koma wosaumbalidwa asadyeko.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Ngati mlendo wokhala pakati panu angafune kuchita nawo mwambo wa chikondwerero cha Paska, cha Yehovachi, amuna onse a mʼnyumba mwake ayenera kuchita mdulidwe. Akatero muzimutenga ngati mbadwa pakati panu. Koma aliyense wosachita mdulidwe asadye Paska.

Onani mutuwo



Eksodo 12:48
12 Mawu Ofanana  

Muzidula khungu lanu; ndipo chidzakhala chizindikiro cha pangano pakati pa Ine ndi inu.


A masiku asanu ndi atatu azidulidwa mwa inu, ana aamuna onse m'mibadwo mwanu, amene abadwa m'nyumba ndi amene agulidwa ndi ndalama kwa alendo ali onse, wosakhala mwa mbeu zako.


Chisapezeke chotupitsa m'nyumba zanu masiku asanu ndi awiri; pakuti aliyense wakudya kanthu ka chotupitsa, munthuyo adzachotsedwa ku gulu la Israele, angakhale ndiye mlendo kapena wobadwa m'dziko.


Ndipo Yehova anati kwa Mose ndi Aroni, Lemba la Paska ndi ili: mwana wa mlendo aliyense asadyeko;


Pakuti aliyense wa nyumba ya Israele, kapena wa alendo ogonera mu Israele, wodzisiyanitsa kusatsata Ine, nautsa mafano ake m'mtima mwake, naimika chokhumudwitsa cha mphulupulu yake pamaso pake, nadzera mneneri kudzifunsira kwa Ine, Ine Yehova ndidzamyankha ndekha;


Atero Ambuye Yehova, Palibe mlendo wosadulidwa m'mtima, wosadulidwa m'thupi, alowe m'malo anga opatulika, mwa alendo onse ali pakati pa ana a Israele.


Ndipo kudzachitika kuti muligawe ndi kuchita maere, likhale cholowa chanu, ndi cha alendo akukhala pakati pa inu; ndipo akhale kwa inu ngati obadwa m'dziko mwa ana a Israele, alandire cholowa pamodzi ndi inu mwa mafuko a Israele.


Mlendo wakugonera kwa inu mumuyese pakati pa inu monga wa m'dziko momwemo; umkonde monga udzikonda wekha; popeza munali alendo m'dziko la Ejipito; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


Ndipo mlendo akakhala mwa inu, nakachitira Yehova Paska, azichita monga mwa lemba la Paska, ndi monga mwa chiweruzo chake; lemba likhale limodzi kwa inu, ndi kwa mlendo, ndi kwa wobadwa m'dziko.


Muno mulibe Myuda, kapena Mgriki, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Khristu Yesu.


pamene palibe Mgriki ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, watchedwa wakunja, Msukuti, kapolo, mfulu, komatu Khristu ndiye zonse, ndi m'zonse.