Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 12:46 - Buku Lopatulika

Audye m'nyumba imodzi; usatulukira nayo kubwalo nyama ina; ndipo musathyole fupa lake.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Audye m'nyumba imodzi; usatulukira nayo kubwalo nyama ina; ndipo musathyole fupa lake.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Muzidyera m'nyumba imodzi, musatuluke nayo panja nyamayo, ndipo musaphwanye mafupa ake.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Muzidyera Paska mʼnyumba imodzi. Musatulutse nyama iliyonse kunja kwa nyumba. Musaswe mafupa aliwonse.

Onani mutuwo



Eksodo 12:46
7 Mawu Ofanana  

Iye asunga mafupa ake onse; silinathyoke limodzi lonse.


Mphulupulu idzamupha woipa; ndipo adzawatsutsa kumlandu iwo akudana naye wolungama.


Asasiyeko kufikira m'mawa, kapena kuthyolapo fupa; auchite monga mwa lemba lonse la Paska.


koma pofika kwa Yesu, m'mene anamuona Iye, kuti wafa kale, sanathyole miyendo yake;


Pakuti izi zinachitika, kuti lembo likwaniridwe, Fupa la Iye silidzathyoledwa.


Pakuti monga thupi lili limodzi, nilikhala nazo ziwalo zambiri; koma ziwalo zonse za thupilo, pokhala zambiri, zili thupi limodzi; momwemonso Khristu.