Ndipo mfumu inalamulira anthu onse, kuti, Mchitireni Yehova Mulungu wanu Paska, monga mulembedwa m'buku ili la chipangano.
Eksodo 12:21 - Buku Lopatulika Pamenepo Mose anaitana akulu onse a Israele, nanena nao, Pitani, dzitengereni anaankhosa monga mwa mabanja anu, nimuphere Paska. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Mose anaitana akulu onse a Israele, nanena nao, Pitani, dzitengereni anaankhosa monga mwa mabanja anu, nimuphere Paska. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Mose adaitana atsogoleri onse a Aisraele, naŵauza kuti, “Pitani kasankhuleni mwanawankhosa woyenera pa banja lililonse, ndipo muphe nyama ya Paskayo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Mose anasonkhanitsa akuluakulu onse a Israeli nati, “Pitani msanga kukasankha nkhosa zokwanira pa mabanja anu, ndipo muziphe ngati Paska. |
Ndipo mfumu inalamulira anthu onse, kuti, Mchitireni Yehova Mulungu wanu Paska, monga mulembedwa m'buku ili la chipangano.
Pakuti ansembe ndi Alevi anadziyeretsa pamodzi, anayera onsewo, naphera Paska chifukwa cha ana onse a ndende, ndi abale ao ansembe, ndi iwo okha.
Ndipo muziidya chotero: okwinda m'chuuno, nsapato zanu pa mapazi anu ndodo yanu m'dzanja lanu, ndipo muziidya msanga; ndiye Paska wa Yehova.
Mulankhule ndi gulu lonse la Israele ndi kuti, Tsiku lakhumi la mwezi uno adzitengere munthu yense mwanawankhosa, monga mwa mabanja a atate ao, mwanawankhosa pabanja.
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pita pamaso pa anthu, nutenge pamodzi nawe akulu ena a Israele; nutenge m'dzanja mwako ndodo ija unapanda nayo mtsinje, numuke.
Ndipo Mose anadza, naitana akulu a anthu, nawaikira pamaso pao mau awa onse amene Yehova adamuuza.
Muka, nukasonkhanitse akulu a Israele, nunene nao, Yehova, Mulungu wa makolo anu anandionekera ine, Mulungu wa Abrahamu, Isaki ndi Yakobo, ndi kuti, Ndakuzondani ndithu, ndi kuona chomwe akuchitirani mu Ejipito;
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Undisonkhanitsire amuna makumi asanu ndi awiri mwa akulu a Israele, amene uwadziwa kuti ndiwo akulu a anthu, ndi akapitao ao; nubwere nao ku chihema chokomanako, kuti aimeko pamodzi ndi iwe.
namwa onse chakumwa chauzimu chimodzimodzi; pakuti anamwa mwa thanthwe lauzimu lakuwatsata; koma thanthwelo ndiye Khristu.
Ndi chikhulupiriro anachita Paska, ndi kuwaza kwa mwazi, kuti wakuononga ana oyamba angawakhudze iwo.
Ndipo ana a Israele anamanga misasa ku Giligala; nachita Paska tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi, madzulo, m'zidikha za Yeriko.