Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 12:22 - Buku Lopatulika

22 Ndipo muzitenga mpukutu wa hisope, ndi kuuviika m'mwazi uli m'mbale, ndi kupaka mwazi uli m'mbalemo pa mphuthu ya pamwamba ndi pambali; koma inu, asatuluke munthu pakhomo pa nyumba yake kufikira m'mawa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Ndipo muzitenga mpukutu wa hisope, ndi kuuviika m'mwazi uli m'mbale, ndi kupaka mwazi uli m'mbalemo pa mphuthu ya pamwamba ndi pambali; koma inu, asatuluke munthu pakhomo pa nyumba yake kufikira m'mawa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Mutenge nthambi ya kachitsamba ka hisope, muiviike m'magazi amene mwaŵathira m'mbale. Tsono muwaze magaziwo pa mphuthu ziŵiri za chitsekozo ndi pamwamba pa chitseko. Wina aliyense asatuluke m'nyumba mwake mpaka m'maŵa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Mutengenso nthambi ya chitsamba cha hisope, muchiviyike mʼmagazi amene mwawayika mʼbeseni ndipo muwaze ena mwa magaziwo pamwamba ndi mʼmbali mwa mphuthu za chitseko. Palibe aliyense wa inu amene adzatuluke mʼnyumba yake mpaka mmawa.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 12:22
13 Mawu Ofanana  

Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera; munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbuu woposa matalala.


Ndipo azitengako mwazi, naupake pa mphuthu za mbali ndi ya pamwamba m'nyumba zimene adyeramo.


Idzani, anthu anga, lowani m'zipinda mwanu, nimutseke pamakomo panu; nimubisale kanthawi kufikira mkwiyo utapita.


ndi munthu woyera atenge hisope, namviike m'madzimo, ndi kuwawaza pahema ndi pa zotengera zonse, ndi pa anthu anali pomwepo, ndi pa iye wakukhudza fupa, kapena wophedwa, kapena wakufa, kapena manda.


Ndipo pamene anaimba nyimbo, anatuluka kunka kuphiri la Azitona.


Ndi chikhulupiriro anachita Paska, ndi kuwaza kwa mwazi, kuti wakuononga ana oyamba angawakhudze iwo.


ndi kwa Yesu Nkhoswe ya chipangano chatsopano, ndi kwa mwazi wa kuwaza wakulankhula chokoma choposa mwazi wa Abele.


Ndipo chingakhale chipangano choyambachi chinali nazo zoikika za kulambira, ndi malo opatulika a padziko lapansi.


koposa kotani nanga mwazi wa Khristu amene anadzipereka yekha wopanda chilema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa chikumbumtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?


Pakuti pamene Mose adalankhulira anthu onse lamulo lililonse monga mwa chilamulo, anatenga mwazi wa anaang'ombe ndi mbuzi, pamodzi ndi madzi ndi ubweya wofiira ndi hisope, nawaza buku lomwe, ndi anthu onse,


Ndipo kudzakhala kuti aliyense akadzatuluka pa khomo la nyumba yako kubwalo, imfa imeneyi ndi yake, tilibe kupalamula ife; koma aliyense adzakhala ndi iwe m'nyumba, likamfikira dzanja, imfa imeneyi ndi yathu.


monga mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m'chiyeretso cha Mzimu, chochitira chimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Khristu: Chisomo, ndi mtendere zichulukire inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa