Eksodo 12:10 - Buku Lopatulika Ndipo musasiyako kufikira m'mawa; koma yotsalira kufikira m'mamawayo muipsereze ndi moto. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo musasiyako kufikira m'mawa; koma yotsalira kufikira m'mamawayo muipsereze ndi moto. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Musasiyeko nyama ina mpaka m'maŵa, motero ina ikatsalako, muitenthe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Musadzasiye nyama ina mpaka mmawa, ngati ina idzatsala mpaka mmawa, mudzayitenthe. |
Usapereka mwazi wa nsembe yanga pamodzi ndi mkate wa chotupitsa; ndi mafuta a madyerero anga asagonamo kufikira m'mawa.
Ndipo ikatsalako nyama yodzaza manja, kapena mkate kufikira m'mawa, pamenepo utenthe zotsalazo ndi moto; asazidye popeza nchopatulika ichi.
Usapereke mwazi wa nsembe yanga yophera pamodzi ndi mkate wachotupitsa; ndi nsembe yophera ya chikondwerero cha Paska asaisiye kufikira m'mawa.
Tsiku lomwelo mwaipha, ndi m'mawa mwake muidye; ngati katsalirako kanthu tsiku lachitatu, muzikatentha ndi moto.
Asasiyeko kufikira m'mawa, kapena kuthyolapo fupa; auchite monga mwa lemba lonse la Paska.