Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 12:10 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Musadzasiye nyama ina mpaka mmawa, ngati ina idzatsala mpaka mmawa, mudzayitenthe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

10 Ndipo musasiyako kufikira m'mawa; koma yotsalira kufikira m'mamawayo muipsereze ndi moto.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo musasiyako kufikira m'mawa; koma yotsalira kufikira m'mamawayo muipsereze ndi moto.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Musasiyeko nyama ina mpaka m'maŵa, motero ina ikatsalako, muitenthe.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 12:10
9 Mawu Ofanana  

Ndipo Mose anawawuza kuti, “Wina aliyense asasunge mpaka mmawa.”


“Musapereke magazi anyama ngati nsembe kwa Ine pamodzi ndi chilichonse chimene chili ndi yisiti. “Ndipo musasunge mafuta anyama yansembe ya pa chikondwerero mpaka mmawa.


Ndipo ngati nyama ina ya nkhosa ya pamwambo wodzoza ansembe kapena buledi zatsala mpaka mmawa, muziwotche, asazidye chifukwa ndi zopatulika.


“Musapereke magazi anyama ngati nsembe kwa Ine pamodzi ndi chilichonse chimene chili ndi yisiti, ndipo musasunge nsembe ya pa Chikondwerero cha Paska mpaka mmawa.


Nsembe izidyedwa tsiku lomwe mwayiperekalo kapena mmawa mwake. Chilichonse chotsala mpaka tsiku lachitatu chiyenera kutenthedwa.


Muyidye pa tsiku lomwelo, wosasiyako ina mpaka mmawa. Ine ndine Yehova.


Iwo asasiye nyama ina iliyonse mpaka mmawa. Asaswe mafupa aliwonse. Pamene akuchita chikondwerero cha Paska, atsate malangizo onse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa