Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao nanena naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Ukana kudzichepetsa pamaso panga kufikira liti? Lola anthu anga amuke, akanditumikire;
Eksodo 10:4 - Buku Lopatulika pakuti ukakana kulola anthu anga amuke, taona, mawa ndidzafikitsa dzombe m'dziko lako; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pakuti ukakana kulola anthu anga amuke, taona, mawa ndidzafikitsa dzombe m'dziko lako; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ukakanabe kuŵalola kuti apite, ndikugwetsera dzombe maŵa m'dziko mwako. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngati ukana kuwalola, ndigwetsa dzombe mʼdziko lako lino mawa. |
Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao nanena naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Ukana kudzichepetsa pamaso panga kufikira liti? Lola anthu anga amuke, akanditumikire;
ndipo lidzakuta nkhope ya dziko, kotero kuti palibe munthu adzakhoza kuona dziko; ndipo lidzadya zotsalira zidapulumuka, zidatsalira inu pamatalala, ndipo lidzadya mtengo uliwonse wokuphukirani kuthengo;
Ndipo ndanena ndi iwe, Mlole mwana wanga amuke, kuti anditumikire Ine; koma wakana kumlola kuti asamuke; taona, Ine ndidzamupha mwana wako wamwamuna, mwana wako woyamba.
Ndipo pambuyo pake Mose ndi Aroni analowa nanena ndi Farao, Atero Yehova, Mulungu wa Israele, Lola anthu anga apite, kundichitira madyerero m'chipululu.
Ndipo anati, Mawa. Nati Mose, Kukhale monga mau anu, kuti muziwe, kuti palibe wina wonga Yehova Mulungu wathu.
Ndipo ndidzaika chosiyanitsa pakati pa anthu anga ndi anthu ako; mawa padzakhala chizindikiro ichi.
Taona, mawa monga nthawi ino ndidzavumbitsa mvumbi wa matalala, sipadakhale unzake mu Ejipito kuyambira tsiku lija lidakhazikika kufikira lero lino.
Ndipo ndidzakubwezerani zaka zidazidya dzombe, ndi chirimamine, ndi anoni, ndi chimbalanga, gulu langa lalikulu la nkhondo, limene ndinalitumiza pakati pa inu.
Mudzatuluka nazo mbeu zambiri kumunda, koma mudzakolola pang'ono; popeza dzombe lidzazitha.
Ndipo mu utsimo mudatuluka dzombe padziko, ndipo analipatsa ilo mphamvu monga zinkhanira za dziko zili ndi mphamvu.