Ndipo Nowa anamanga guwa la nsembe la Yehova; natengapo nyama zodyedwa zonse ndi mbalame zodyedwa zonse napereka nsembe zopsereza paguwapo.
Eksodo 10:25 - Buku Lopatulika Koma Mose anati, Mutipatsenso m'dzanja mwathu nsembe zophera ndi nsembe zopsereza, kuti timkonzere Yehova Mulungu wathu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma Mose anati, Mutipatsenso m'dzanja mwathu nsembe zophera ndi nsembe zopsereza, kuti timkonzere Yehova Mulungu wathu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mose adati, “Tsonotu muyenera kutipatsa ndinu zokaperekera nsembe zopsereza kwa Chauta, Mulungu wathu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Mose anati, “Ndiye inu mutipatse nsembe zopsereza zoti tikapereke kwa Yehova Mulungu wathu. |
Ndipo Nowa anamanga guwa la nsembe la Yehova; natengapo nyama zodyedwa zonse ndi mbalame zodyedwa zonse napereka nsembe zopsereza paguwapo.
Ndipo Farao anaitana Mose, nati, Mukani, tumikirani Yehova; nkhosa zanu ndi ng'ombe zanu zokha zitsale; mumuke nao ana anu aang'ononso.
Zoweta zathu zomwe tidzapita nazo; chosatsala chiboda chimodzi; pakuti mwa izo tiyenera kutenga zakutumikira nazo Yehova Mulungu wathu; ndipo tisanafikeko, sitidziwa umo tidzamtumikira Yehova.
Undiumbire guwa la nsembe ladothi, nundiphere pomwepo nsembe zako zopsereza, ndi nsembe zako zamtendere, nkhosa zako ndi ng'ombe zako; paliponse ndikumbukiritsa anthu dzina langa ndidzakudzera ndi kukudalitsa.
Ndipo Aroni anakweza dzanja lake kulozera anthu, nawadalitsa; natsika kuja anapereka nsembe yauchimo, ndi nsembe yopsereza, ndi nsembe zoyamika.