Ndipo Yehova anabweza mphepo yolimbatu ya kumadzulo, imene inapita nalo dzombe niliponya mu Nyanja Yofiira: silinatsale dzombe limodzi pakati pa malire onse a Ejipito.
Eksodo 10:18 - Buku Lopatulika Ndipo anatuluka kwa Farao, napemba Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anatuluka kwa Farao, napemba Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mose adachoka kwa Farao kuja, nakapemphera kwa Chauta. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose anachoka kwa Farao nakapemphera kwa Yehova. |
Ndipo Yehova anabweza mphepo yolimbatu ya kumadzulo, imene inapita nalo dzombe niliponya mu Nyanja Yofiira: silinatsale dzombe limodzi pakati pa malire onse a Ejipito.
Ndipo Mose ndi Aroni anatuluka kwa Farao; ndi Mose anafuulira kwa Yehova kunena za achule amene adawaika pa Farao.
Pamenepo Farao anaitana Mose ndi Aroni, nati, Mundipembere Yehova, kuti andichotsere ine ndi anthu anga achulewo; ndipo ndidzalola anthu amuke, kuti amphere Yehova nsembe.
Koma Mose anati kwa Farao, Ulemu ndi wanu, wa ine ai; ndipembere inu ndi anyamata anu ndi anthu anu liti, kuti aonongeke achulewo, achokere inu ndi nyumba zanu, atsale m'mtsinje mokha?
Pamenepo anthu anafuulira kwa Mose; ndi Mose anapemphera kwa Yehova, ndi motowo unazima.