Pamene Yehova anaona kuti anamuda Leya, anatsegula m'mimba mwake; koma Rakele anali wouma.
Eksodo 1:1 - Buku Lopatulika Ndipo maina a ana a Israele, amene analowa mu Ejipito ndi Yakobo ndi awa, analowa munthu ndi banja lake: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo maina a ana a Israele, amene analowa m'Ejipito ndi Yakobo ndi awa, analowa munthu ndi banja lake: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Naŵa ana a Yakobe amene adapita ku Ejipito pamodzi ndi Yakobeyo ndi mabanja ao omwe: Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Awa ndi mayina a ana a Israeli amene anapita ku Igupto pamodzi ndi Yakobo abambo awo, aliyense ndi banja lake: |
Pamene Yehova anaona kuti anamuda Leya, anatsegula m'mimba mwake; koma Rakele anali wouma.
Ndipo pakutsirizika iye, pakuti anamwalira, anamutcha dzina lake Benoni; koma atate wake anamutcha Benjamini.
ndi ana aamuna a Yosefe, amene anambadwira iye mu Ejipito ndiwo anthu awiri; anthu onse a mbumba ya Yakobo, amene analowa mu Ejipito anali makumi asanu ndi awiri.
maina asanu ndi limodzi pamwala wina, ndi maina asanu ndi limodzi otsala pamwala unzake, mwa kubadwa kwao.
Maina a mafuko tsono ndi awa: Kuyambira nsonga ya kumpoto, ku mbali ya njira ya ku Hetiloni, polowera ku Hamati, Hazara-Enani ku malire a Damasiko kumpoto, ku mbali ya ku Hamati; ndi mbali zake zilinge kum'mawa ndi kumadzulo; Dani akhale nalo gawo limodzi.