Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 1:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Awa ndi mayina a ana a Israeli amene anapita ku Igupto pamodzi ndi Yakobo abambo awo, aliyense ndi banja lake:

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Ndipo maina a ana a Israele, amene analowa mu Ejipito ndi Yakobo ndi awa, analowa munthu ndi banja lake:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo maina a ana a Israele, amene analowa m'Ejipito ndi Yakobo ndi awa, analowa munthu ndi banja lake:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Naŵa ana a Yakobe amene adapita ku Ejipito pamodzi ndi Yakobeyo ndi mabanja ao omwe:

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 1:1
15 Mawu Ofanana  

Pamene Mulungu anaona kuti Yakobo sankamukonda Leya kwambiri, Iye analola kuti Leya uja akhale ndi ana, ndi kuti Rakele akhale wosabala.


Tsono pamene Rakele ankapuma wefuwefu (popeza ankamwalira) iye anatcha mwana uja kuti Beni-Oni. Koma abambo ake anamutcha kuti Benjamini.


Pophatikiza ana awiri a Yosefe obadwira ku Igupto, anthu a pa banja la Yakobo amene anapita ku Igupto, onse pamodzi analipo 70.


Rubeni, Simeoni, Levi, Yuda;


Mayina asanu ndi limodzi akhale pa mwala umodzi, ndipo mayina asanu ndi limodzi pa mwala winawo motsata mabadwidwe awo.


“Nawa mayina a mafuko a Israeli: Dani adzakhala ndi chigawo chimodzi kuyambira kumalire akumpoto kuchokera ku nyanja kudzera ku Hetiloni mpaka ku chipata cha Hamati, kukafika ku Hazari-Enani, mzinda umene uli kumpoto kwa malire a Damasiko oyangʼanana ndi Hamati, kuchokera mʼchigawo chimodzi kummawa mpaka kumadzulo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa