Danieli 6:2 - Buku Lopatulika ndi akuyang'anira iwo akulu atatu, woyamba wao ndi Daniele; kuti akalonga awa adziwerengere kwa iwo, ndi kuti za mfumu zisasoweke. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi akuyang'anira iwo akulu atatu, woyamba wao ndi Daniele; kuti akalonga awa adziwerengere kwa iwo, ndi kuti za mfumu zisasoweke. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndikusankha nduna zazikulu zitatu kuti ziwayangʼanire ndipo imodzi mwa ndunazo anali Danieli. Akalongawo amayangʼaniridwa ndi nduna zazikuluzo kuti zinthu za mfumu zisawonongeke. |
pakuti tagulitsidwa; ine ndi anthu a mtundu wanga, kuti ationonge, atiphe, natipulule. Koma tikadagulitsidwa tikhale akapolo ndi adzakazi, ndikadakhala chete; chinkana wosautsa sakadatha kubwezera kusowa kwa mfumu.
Koma ndamva ine za iwe, kuti ukhoza kutanthauzira mau, ndi kumasula mfundo; tsono ukakhoza kuwerenga lembalo, ndi kundidziwitsa kumasulira kwake, udzavekedwa chibakuwa, ndi unyolo wagolide m'khosi mwako; nudzakhala wolamulira wachitatu mu ufumuwo.
Pamenepo Belisazara analamulira, ndipo anaveka Daniele chibakuwa, ndi unyolo wagolide m'khosi mwake, nalalikira za iye kuti ndiye wolamulira wachitatu mu ufumumo.
Nifuulitsa mfumu abwere nao openda, Ababiloni, ndi alauli. Mfumu inalankhula, niti kwa anzeru a ku Babiloni, Aliyense amene adzawerenga lemba ili, nadzandifotokozera kumasulira kwake, adzavekedwa chibakuwa, ndi unyolo wagolide m'khosi mwake, nadzakhala wolamulira wachitatu mu ufumuwu.
Kudamkomera Dariusi kuikira ufumuwo akalonga zana limodzi mphambu makumi awiri akhale m'madera onse a ufumu;
Chifukwa chake Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, mfumu, amene anafuna kuwerengera nao akapolo ake.
Ndipo anamuitana, nati kwa iye, Ichi ndi chiyani ndikumva za iwe? Undiwerengere za ukapitao wako; pakuti sungathe kukhalabe kapitao.
Chifukwa chake Yehova Mulungu wa Israele akuti, Ndinaterodi kuti banja lako ndi banja la kholo lako lidzayenda pamaso panga nthawi zonse; koma tsopano Yehova ati, Chikhale kutali ndi Ine; popeza amene andilemekeza Ine, Inenso ndidzawalemekeza iwowa, ndipo akundipeputsa Ine, adzapeputsidwa.