koma izi ziwiri zidzakugwera mwadzidzidzi, tsiku limodzi kumwalira kwa ana ndi umasiye zidzakugwera; mokwanira monse, pakati pa maphenda ako ambirimbiri.
Danieli 5:30 - Buku Lopatulika Usiku womwewo Belisazara mfumu ya Ababiloni anaphedwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Usiku womwewo Belisazara mfumu ya Ababiloni anaphedwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Usiku womwewo Belisazara, mfumu ya anthu a ku Babuloni, inaphedwa, |
koma izi ziwiri zidzakugwera mwadzidzidzi, tsiku limodzi kumwalira kwa ana ndi umasiye zidzakugwera; mokwanira monse, pakati pa maphenda ako ambirimbiri.
Ndakutchera iwe msampha, ndi iwenso wagwidwa, iwe Babiloni, ndipo sunadziwe, wapezeka, ndiponso wagwidwa, chifukwa walimbana ndi Yehova.
Nolani mivi; gwirani zolimba zikopa; Yehova waukitsa mtima wa mafumu a Amedi; chifukwa alingalirira Babiloni kuti amuononge; pakuti ndi kubwezera chilango kwa Yehova; kubwezera chilango chifukwa cha Kachisi wake.
Wamtokoma mmodzi adzathamanga kukakomana ndi mnzake, ndi mthenga mmodzi kukomana ndi mnzake, kukauza mfumu ya ku Babiloni kuti mzinda wake wagwidwa ponsepo;
Pamene atentha, ndidzakonza madyerero ao, ndidzawaledzeretsa, kuti asangalale, agone chigonere, asanyamuke, ati Yehova.
Ndipo ndidzaledzeretsa akulu ake ndi anzeru ake, akazembe ake ndi ziwanga zake, ndi anthu ake olimba; ndipo adzagona chigonere, sadzanyamuka, ati Mfumu, dzina lake ndi Yehova wa makamu.
Chifukwa chake tsono, adzatengedwa ndende ndi oyamba kutengedwa ndende; ndi phokoso la iwo odzithinula lidzapita.