Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 51:11 - Buku Lopatulika

11 Nolani mivi; gwirani zolimba zikopa; Yehova waukitsa mtima wa mafumu a Amedi; chifukwa alingalirira Babiloni kuti amuononge; pakuti ndi kubwezera chilango kwa Yehova; kubwezera chilango chifukwa cha Kachisi wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Nolani mivi; gwirani zolimba zikopa; Yehova waukitsa mtima wa mafumu a Amedi; chifukwa alingalirira Babiloni kuti amuononge; pakuti ndi kubwezera chilango kwa Yehova; kubwezera chilango chifukwa cha Kachisi wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 “Songolani mivi, tengani zishango.” Chauta wautsa mitima ya mafumu a Amedi, poti cholinga chake nchoti aononge Babiloni. Afuna kumlipsira chifukwa choononga Nyumba yake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 “Yehova wadzutsa mitima ya mafumu a Amedi, popeza cholinga chake ndi kuwononga Babuloni. Motero adzalipsira Ababuloni chifukwa chowononga Nyumba yake. Ndiye Yehova akuti, ‘Nolani mivi, tengani zishango.’

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 51:11
39 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anamuutsira Solomoni mdani, ndiye Hadadi Mwedomu; iyeyo anali wa mbumba ya mfumu ya ku Edomu.


Ndipo Mulungu anamuutsira mdani wina, ndiye Rezoni mwana wa Eliyada, amene adathawa mbuye wake Hadadezere mfumu ya ku Zoba.


Ndipo Mulungu wa Israele anautsa mzimu wa Pulo mfumu ya Asiriya, ndi mzimu wa Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, ndiye anawatenga ndende; ndiwo Arubeni, ndi Agadi, ndi hafu la fuko la Manase, nafika nao ku Hala, ndi Habori, ndi Hara ndi ku mtsinje wa Gozani, mpaka lero lino.


Chaka choyamba tsono cha Kirusi mfumu ya Persiya, kuti akwaniridwe mau a Yehova pakamwa pa Yeremiya, Yehova anautsa mzimu wa Kirusi mfumu ya Persiya, kuti abukitse mau mu ufumu wake wonse, nawalembenso, ndi kuti,


Chaka choyamba tsono cha Kirusi mfumu ya ku Persiya, kuti akwaniridwe mau a Yehova m'kamwa mwa Yeremiya, Yehova anautsa mzimu wa Kirusi, kuti abukitse mau mu ufumu wake wonse, nawalembenso, ndi kuti,


Ndipo Yehova wa makamu adzamuutsira chikoti, monga m'kuphedwa kwa Midiyani pa thanthwe la Orebu; ndipo chibonga chake chidzakhala pamwamba pa nyanja, ndipo adzaisamula monga anachitira Ejipito,


Masomphenya ovuta aonetsedwa kwa ine; wogula malonda wonyenga amangonyenga, ndi wofunkha amangofunkha. Kwera Elamu iwe; zunguniza Mediya iwe; kuusa moyo kwake konse ndakutonthoza.


Iwo akonza pa gome lodyera, aika alonda, adya, namwa; ukani, akalonga inu, dzozani mafuta chikopa.


Ndautsa wina wakuchokera kumpoto; ndipo iye wafika wakuchokera potuluka dzuwa, amene atchula dzina langa; ndipo iye adzafika pa olamulira, monga matope, ndi monga muumbi aponda dothi la mbiya.


Atero Yehova kwa wodzozedwa wake kwa Kirusi, amene dzanja lake lamanja ndaligwiritsa, kuti agonjetse mitundu ya anthu pamaso pake, ndipo ndidzamasula m'chuuno mwa mafumu; atsegule zitseko pamaso pake, ndi zipata sizidzatsekedwa:


Ine ndili Yehova, ndipo palibe winanso; popanda Ine palibe Mulungu; ndidzakumanga m'chuuno, ngakhale sunandidziwe;


ndiitana mbalame yolusa kuchokera kum'mawa, ndiye munthu wa uphungu wanga, kuchokera kudziko lakutali; inde, ndanena, ndidzachionetsa; ndinatsimikiza mtima, ndidzachichitanso.


ndi mafumu onse a Zimiri, ndi mafumu onse a Elamu, ndi mafumu onse a ku Mediya,


Konzani chikopa ndi lihawo, nimuyandikire kunkhondo.


Mangani akavalo, bwerani, inu apakavalo, imani ndi zisoti zazitsulo; tuulani nthungo zanu, valani malaya achitsulo.


Kwerani, inu akavalo; chitani misala, inu magaleta, atuluke amphamvu; Akusi ndi Aputi, ogwira chikopa; ndi Aludi, amene agwira ndi kukoka uta.


Yehova watsegula pa nyumba ya zida zake, ndipo watulutsa zida za mkwiyo wake; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, ali ndi ntchito m'dziko la Ababiloni.


Pakuti mtundu wa anthu udzatuluka kumpoto kudzamenyana naye, udzachititsa dziko lake bwinja, losakhalamo anthu; athawa, apita, anthu ndi nyama.


Chifukwa chake tamvani uphungu wa Yehova, umene waupangira pa Babiloni; ndi zimene walingirira dziko la Ababiloni; ndithu adzawakoka, ana aang'ono a zoweta; ndithu adzayesa busa lao bwinja pamodzi nao.


Pakuti, taonani, ndidzabukitsa ndidzafikitsa kudzamenyana ndi Babiloni msonkhano wa mitundu yaikulu kuchokera kudziko la kumpoto; ndipo adzaguba pomenyana ndi iye; kumeneko Babiloni adzachotsedwa; mivi yao idzakhala ngati ya munthu wamaluli wamphamvu; yosabwera chabe.


Muwakwezere mbendera makoma a Babiloni, mulimbikitse ulonda, muike alonda, mupangiretu olalira, pakuti Yehova waganiziratu ndi kuchita chomwe ananena za okhala mu Babiloni.


Ndipo ndidzabwezera Babiloni ndi okhala mu Kasidi zoipa zao zonse anazichita mu Ziyoni pamaso panu, ati Yehova.


Wokhala mu Ziyoni adzati, Chiwawa anandichitira ine ndi thupi langa chikhale pa Babiloni; nadzati Yerusalemu, Mwazi wanga ukhale pa okhala mu Kasidi.


Chifukwa chake Yehova atero: Taona, ndidzanenera iwe mlandu wako, ndidzawabwezera chilango chifukwa cha iwe; ndidzaphwetsa nyanja yake, ndidzaphwetsa chitsime chake.


Usiku womwewo Belisazara mfumu ya Ababiloni anaphedwa.


Sulani makasu anu akhale malupanga, ndi zikwakwa zanu zikhale nthungo; wofooka anene, Ndine wamphamvu.


Mulalikire ichi mwa amitundu, mukonzeretu nkhondo; utsani amuna amphamvu; amuna onse a nkhondo ayandikire nakwere.


Ndipo ndidzadzetsa kwa inu lupanga lakuchita chilango cha chipangano; kotero kuti mudzasonkhanidwa m'mizinda mwanu; ndipo ndidzatumiza mliri pakati pa inu; ndipo mudzaperekedwa m'manja mwa mdani.


Ndipo mliri umene Yehova adzakantha nao mitundu yonse ya anthu imene idathira nkhondo pa Yerusalemu ndi uwu: nyama yao idzaonda akali chilili pa mapazi ao, ndi maso ao adzapuwala m'funkha mwao, ndi lilime lao lidzanyala m'kamwa mwao.


Pakuti ndidzasonkhanitsa amitundu onse alimbane ndi Yerusalemu; ndipo mzindawo udzalandidwa, ndi nyumba zidzafunkhidwa, ndi akazi adzakakamizidwa; ndi limodzi la magawo awiri la mzinda lidzatuluka kunka kundende, koma anthu otsala sadzaonongeka m'mzindamo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa