Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 6:7 - Buku Lopatulika

7 Chifukwa chake tsono, adzatengedwa ndende ndi oyamba kutengedwa ndende; ndi phokoso la iwo odzithinula lidzapita.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Chifukwa chake tsono, adzatengedwa ndende ndi oyamba kutengedwa ndende; ndi phokoso la iwo odzithinula lidzapita.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Nchifukwa chake mudzatsogola ndinu kupita ku ukapolo, ndipo maphwando ndi zikondwerero zidzakutherani.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Nʼchifukwa chake inu mudzakhala mʼgulu la anthu oyamba kupita ku ukapolo; maphwando ndi zikondwerero zanu zidzatheratu.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 6:7
17 Mawu Ofanana  

ngati mfumu indikomera mtima, ngatinso chakomera mfumu kupereka pempho langa ndi kuchita chofuna ine, adze mfumu ndi Hamani ku madyerero ndidzawakonzera; ndipo mawa ndidzachita monga yanena mfumu.


Mtima wanga uguguda, mantha andiopsetsa ine; chizirezire chimene ndinachikhumba chandisandukira kunthunthumira.


Kusangalala kwa mangaka kwalekeka, phokoso la iwo amene asekera litha, kukondwa kwa mngoli kwalekeka.


Usiku womwewo Belisazara mfumu ya Ababiloni anaphedwa.


Ndipo mudzatulukira popasuka linga, yense m'tsogolo mwake, ndi kutayika ku Harimoni, ati Yehova.


M'mwemo ndidzakutengani kunka nanu kundende kutsogolo kwa Damasiko, ati Yehova, amene dzina lake ndiye Mulungu wa makamu.


koma musamafuna Betele, kapena kumalowa mu Giligala; musamapita ku Beereseba; pakuti Giligala adzalowadi m'ndende, ndi Betele adzasanduka chabe.


Pakuti atero Amosi, Yerobowamu adzafa ndi lupanga, ndi Israele adzatengedwadi ndende, kuchoka m'dziko lake.


chifukwa chake atero Yehova, Mkazi wako adzakhala wadama m'mzinda, ndi ana ako aamuna ndi aakazi adzagwa ndi lupanga, ndi dziko lako lidzagawanidwa ndi kuyesa chingwe, ndi iwe mwini udzafa m'dziko lodetsedwa; ndipo Israele adzatengedwadi ndende kuchoka m'dziko lake.


Pakuti chinkana akunga minga yoyangayanga, naledzera nacho choledzeretsa chao, adzathedwa konse ngati chiputu chouma.


Ndipo adzagwa ndi lupanga lakuthwa, nadzagwidwa ndende kunka kumitundu yonse ya anthu; ndipo mapazi a anthu akunja adzapondereza Yerusalemu kufikira kuti nthawi zao za anthu akunja zakwanira.


Mudzabala ana aamuna ndi aakazi, osakhala nao, popeza adzalowa ukapolo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa