Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Danieli 4:12 - Buku Lopatulika

Masamba ake anali okoma, ndi zipatso zake zinachuluka, ndi m'menemo munali zakudya zofikira onse, nyama zakuthengo zinatsata mthunzi wake, ndi mbalame za m'mlengalenga zinafatsa m'thambi zake, ndi nyama zonse zinadyako.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Masamba ake anali okoma, ndi zipatso zake zinachuluka, ndi m'menemo munali zakudya zofikira onse, nyama za kuthengo zinatsata mthunzi wake, ndi mbalame za m'mlengalenga zinafatsa m'thambi zake, ndi nyama zonse zinadyako.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masamba ake anali okongola, zipatso zinali zochuluka, ndipo mu mtengomo munali chakudya chokwanira anthu onse. Zirombo zakuthengo zimapeza mthunzi mʼmunsi mwake, ndipo mbalame zamlengalenga zimakhala pa nthambi zake: Cholengedwa chilichonse chinkadya za mu mtengowu.

Onani mutuwo



Danieli 4:12
13 Mawu Ofanana  

Awachotsera akulu a anthu a padziko mtima wao, nawasokeretsa m'chipululu chopanda njira.


Pakuti akaulikha mtengo pali chiyembekezo kuti udzaphukanso, ndi kuti nthambi yake yanthete siidzasowa.


Koma pa mnunkho wa madzi udzaphuka, nudzaswa nthambi ngati womera.


Wodzozedwa wa Yehova, ndiye mpweya wa m'mphuno mwathu, anagwidwa m'maenje ao; amene tinanena kuti, Tidzakhala m'mthunzi mwake pakati pa amitundu,


paphiri lothuvuka la Israele ndidzaioka, ndipo idzaphuka nthambi ndi kubala zipatso, nidzakhala mkungudza wokoma, ndi m'munsi mwake mudzakhala mbalame zilizonse za mapiko aliwonse; mu mthunzi wa nthambi zake zidzabindikira.


Iwonso anatsika naye kumanda kwa iwo ophedwa ndi lupanga, ndiwo amene adakhala dzanja lake okhala mumthunzi mwake pakati pa amitundu.


Anafuulitsa, natero, Likhani mtengowo, sadzani nthambi zake, yoyolani masamba ake, mwazani zipatso zake, nyama zakuthengo zichoke pansi pake, ndi mbalame pa nthambi zake.


kamene kakhaladi kakang'ono koposa mbeu zonse, koma katakula, kali kakakulu kuposa zitsamba zonse, nukhala mtengo, kotero kuti mbalame za mlengalenga zimadza, nkubindikira mu nthambi zake.


Koma za tsiku ilo, kapena nthawi yake sadziwa munthu, angakhale angelo mu Mwamba, angakhale Mwana, koma Atate ndiye.


koma pamene ifesedwa, imera nkukula koposa zitsamba zonse, nkukhala ndi nthambi zazikulu; kotero kuti mbalame za m'mlengalenga zikhoza kubindikira mumthunzi mwake.


Ufanana ndi kambeu kampiru, kamene munthu anatenga, nakaponya m'munda wakewake, ndipo kanamera, kanakula mtengo; ndi mbalame za m'mlengalenga zinabindikira mu nthambi zake.