Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 4:12 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Masamba ake anali okongola, zipatso zinali zochuluka, ndipo mu mtengomo munali chakudya chokwanira anthu onse. Zirombo zakuthengo zimapeza mthunzi mʼmunsi mwake, ndipo mbalame zamlengalenga zimakhala pa nthambi zake: Cholengedwa chilichonse chinkadya za mu mtengowu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

12 Masamba ake anali okoma, ndi zipatso zake zinachuluka, ndi m'menemo munali zakudya zofikira onse, nyama zakuthengo zinatsata mthunzi wake, ndi mbalame za m'mlengalenga zinafatsa m'thambi zake, ndi nyama zonse zinadyako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Masamba ake anali okoma, ndi zipatso zake zinachuluka, ndi m'menemo munali zakudya zofikira onse, nyama za kuthengo zinatsata mthunzi wake, ndi mbalame za m'mlengalenga zinafatsa m'thambi zake, ndi nyama zonse zinadyako.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 4:12
13 Mawu Ofanana  

Iye amalanda nzeru za atsogoleri a dziko lapansi; amawayendetsa mʼthengo mopanda njira.


“Mtengo uli nacho chiyembekezo: ngati wadulidwa, udzaphukiranso ndipo nthambi zake sizidzaleka kuphukira.


koma pamene chinyontho chafika udzaphukira ndipo udzaphuka nthambi ngati mtengo wanthete.


Wodzozedwa wa Yehova, mpweya wathu wotipatsa moyo, anakodwa mʼmisampha yawo. Tinaganiza kuti tidzakhala pansi pa mthunzi wake pakati pa mitundu ya anthu.


Ndidzayidzaladi pa phiri lalitali la Israeli. Idzaphuka nthambi ndi kubereka zipatso. Choncho idzasanduka mkungudza wamphamvu. Mbalame za mtundu uliwonse zidzamanga zisa zawo mʼmenemo; zidzapeza malo okhala mu mthunzi wa nthambi zake.


Amene ankakhala mu mthunzi wake, amene ankayanjana nawo, iwonso anapita nawo pamodzi ku manda, kukakhala pamodzi ndi amene anaphedwa ndi lupanga pakati pa mitundu ya anthu.


Anayankhula mofuwula kuti, ‘Gwetsa mtengo ndi kusadza nthambi zake; yoyola masamba ake kuti nyama zakuthengo zithawe pa mthunzi pake ndi mbalame zithawe pa nthambi zake.


Ngakhale mbewuyi ndi yayingʼono mwa mbewu zanu zonse za mʼmunda, imakula ndi kukhala mtengo kotero kuti mbalame zamlengalenga zimabwera ndi kupumula mʼnthambi zake.”


“Palibe amene akudziwa za tsikulo kapena nthawi, ngakhale angelo akumwamba, kapena Mwana, koma Atate wokha.


Koma ikadzalidwa, imakula ndi kukhala yayikulu koposa mbewu zina zonse za mʼmunda ndipo mʼnthambi zake zazikulu mbalame zamlengalenga zimadzapuma pa mthunzi wake.”


Uli ngati mbewu ya mpiru, imene munthu anatenga ndi kudzala mʼmunda mwake. Inakula, nʼkukhala mtengo, ndipo mbalame zamlengalenga zinakhala mʼnthambi zake.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa