Mateyu 13:32 - Buku Lopatulika32 kamene kakhaladi kakang'ono koposa mbeu zonse, koma katakula, kali kakakulu kuposa zitsamba zonse, nukhala mtengo, kotero kuti mbalame za mlengalenga zimadza, nkubindikira mu nthambi zake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201432 kamene kakhaladi kakang'ono koposa mbeu zonse, koma katakula, kali kakakulu kuposa zitsamba zonse, nukhala mtengo, kotero kuti mbalame za mlengalenga zimadza, nizibindikira mu nthambi zake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa32 Ndi yaing'ono kwambiri mukaiyerekeza ndi njere zina zonse. Komabe mbeu yake ikakula, imapambana zitsamba zina zonse. Imasanduka mtengo, mbalame zamumlengalenga nkumabwera kudzamanga zisa pa nthambi zake.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero32 Ngakhale mbewuyi ndi yayingʼono mwa mbewu zanu zonse za mʼmunda, imakula ndi kukhala mtengo kotero kuti mbalame zamlengalenga zimabwera ndi kupumula mʼnthambi zake.” Onani mutuwo |