Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 4:32 - Buku Lopatulika

32 koma pamene ifesedwa, imera nkukula koposa zitsamba zonse, nkukhala ndi nthambi zazikulu; kotero kuti mbalame za m'mlengalenga zikhoza kubindikira mumthunzi mwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 koma pamene ifesedwa, imera nikula koposa zitsamba zonse, nichita nthambi zazikulu; kotero kuti mbalame za m'mlengalenga zikhoza kubindikira mumthunzi mwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Koma akaifesa, imamera, mbeu yake nkukula ndithu kupambana zitsamba zina zonse. Imachita nthambi zazikulu, kotero kuti mbalame zimatha kudzamanga zisa mumthunzi mwake.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Koma ikadzalidwa, imakula ndi kukhala yayikulu koposa mbewu zina zonse za mʼmunda ndipo mʼnthambi zake zazikulu mbalame zamlengalenga zimadzapuma pa mthunzi wake.”

Onani mutuwo Koperani




Marko 4:32
15 Mawu Ofanana  

Mbalame za mlengalenga zifatsa pamenepo, zimaimba pakati pa mitawi.


Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.


Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbee.


Ngati maula pakati pa mitengo ya m'nkhalango, momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana aamuna. Ndinakondwa pakukhala pa mthunzi wake, zipatso zake zinatsekemera m'kamwa mwanga.


Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m'phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzaza ndi odziwa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.


Ndipo munthu adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m'malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m'dziko lotopetsa.


Wodzozedwa wa Yehova, ndiye mpweya wa m'mphuno mwathu, anagwidwa m'maenje ao; amene tinanena kuti, Tidzakhala m'mthunzi mwake pakati pa amitundu,


paphiri lothuvuka la Israele ndidzaioka, ndipo idzaphuka nthambi ndi kubala zipatso, nidzakhala mkungudza wokoma, ndi m'munsi mwake mudzakhala mbalame zilizonse za mapiko aliwonse; mu mthunzi wa nthambi zake zidzabindikira.


kamene kakhaladi kakang'ono koposa mbeu zonse, koma katakula, kali kakakulu kuposa zitsamba zonse, nukhala mtengo, kotero kuti mbalame za mlengalenga zimadza, nkubindikira mu nthambi zake.


Ngati mbeu yampiru, imene ikafesedwa panthaka, ingakhale ichepa ndi mbeu zonse za padziko,


Ndipo ndi mafanizo otere ambiri analankhula nao mau, monga anakhoza kumva;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa