Danieli 2:40 - Buku Lopatulika Ndi ufumu wachinai udzakhala wolimba ngati chitsulo, popeza chitsulo chiphwanya ndi kufoketsa zonse; ndipo monga chitsulo chiswa zonsezi, uwu udzaphwanya ndi kuswa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi ufumu wachinai udzakhala wolimba ngati chitsulo, popeza chitsulo chiphwanya ndi kufoketsa zonse; ndipo monga chitsulo chiswa zonsezi, uwu udzaphwanya ndi kuswa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pomaliza, padzakhala ufumu wachinayi, wolimba ngati chitsulo popeza chitsulo chimaphwanya ndi kutikita chilichonse. Ndipo monga chitsulo chimaphwanya zinthu ndikuteketeratu, choncho udzawononga ndi kuphwanya maufumu ena onse. |
Ndi pambuyo pa inu padzauka ufumu wina wochepa ndi wanu, ndi ufumu wina wachitatu wamkuwa wakuchita ufumu padziko lonse lapansi.
Ndipo umo mudaonera mapazi ndi zala zake, mwina dongo la woumba, mwina chitsulo; ufumuwo udzakhala wogawanika, koma momwemo mudzakhala mphamvu ya chitsulo; popeza mudaona chitsulo chosakanizika ndi dongo.
Pambuyo pake ndinaona m'masomphenya a usiku, ndi kuona chilombo chachinai, choopsa ndi chochititsa mantha, ndi champhamvu choposa, chinali nao mano aakulu achitsulo, chinalusa ndi kuphwanya ndi kupondereza chotsala ndi mapazi ake; chinasiyana ndi zilombo zonse zidachitsogolera; ndipo chinali ndi nyanga khumi.
Ndi mphamvu yake idzakhala yaikulu, koma si mphamvu yakeyake ai, nidzaononga modabwitsa, nidzakuzika, ndi kuchita, ndi kuononga amphamvuwo, ndi anthu opatulikawo.
Ndipo atapita masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri wodzozedwayo adzalikhidwa, nadzakhala wopanda kanthu; ndi anthu a kalonga wakudzayo adzaononga mzinda ndi malo opatulika; ndi kutsiriza kwake kudzakhala kwa chigumula, ndi kufikira chimaliziro kudzakhala nkhondo; chipasuko chalembedweratu.
Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Damasiko, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anapuntha Giliyadi ndi zopunthira zachitsulo;
Ngati timleka Iye kotero, onse adzakhulupirira Iye; ndipo adzadza Aroma nadzachotsa malo athu ndi mtundu wathu.