Danieli 2:41 - Buku Lopatulika41 Ndipo umo mudaonera mapazi ndi zala zake, mwina dongo la woumba, mwina chitsulo; ufumuwo udzakhala wogawanika, koma momwemo mudzakhala mphamvu ya chitsulo; popeza mudaona chitsulo chosakanizika ndi dongo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201441 Ndipo umo mudaonera mapazi ndi zala zake, mwina dongo la woumba, mwina chitsulo; ufumuwo udzakhala wogawanika, koma momwemo mudzakhala mphamvu ya chitsulo; popeza mudaona chitsulo chosanganizika ndi dongo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero41 Ndipo monga munaonera kuti mapazi ndi zala zake zinali za chitsulo chosakaniza ndi dongo, choncho uwu udzakhala ufumu wogawikana; komabe udzakhala ndi mphamvu zina zachitsulo zotikita. Onani mutuwo |
Pambuyo pake ndinaona m'masomphenya a usiku, ndi kuona chilombo chachinai, choopsa ndi chochititsa mantha, ndi champhamvu choposa, chinali nao mano aakulu achitsulo, chinalusa ndi kuphwanya ndi kupondereza chotsala ndi mapazi ake; chinasiyana ndi zilombo zonse zidachitsogolera; ndipo chinali ndi nyanga khumi.