Danieli 2:40 - Buku Lopatulika40 Ndi ufumu wachinai udzakhala wolimba ngati chitsulo, popeza chitsulo chiphwanya ndi kufoketsa zonse; ndipo monga chitsulo chiswa zonsezi, uwu udzaphwanya ndi kuswa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201440 Ndi ufumu wachinai udzakhala wolimba ngati chitsulo, popeza chitsulo chiphwanya ndi kufoketsa zonse; ndipo monga chitsulo chiswa zonsezi, uwu udzaphwanya ndi kuswa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero40 Pomaliza, padzakhala ufumu wachinayi, wolimba ngati chitsulo popeza chitsulo chimaphwanya ndi kutikita chilichonse. Ndipo monga chitsulo chimaphwanya zinthu ndikuteketeratu, choncho udzawononga ndi kuphwanya maufumu ena onse. Onani mutuwo |
Pambuyo pake ndinaona m'masomphenya a usiku, ndi kuona chilombo chachinai, choopsa ndi chochititsa mantha, ndi champhamvu choposa, chinali nao mano aakulu achitsulo, chinalusa ndi kuphwanya ndi kupondereza chotsala ndi mapazi ake; chinasiyana ndi zilombo zonse zidachitsogolera; ndipo chinali ndi nyanga khumi.
Ndipo atapita masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri wodzozedwayo adzalikhidwa, nadzakhala wopanda kanthu; ndi anthu a kalonga wakudzayo adzaononga mzinda ndi malo opatulika; ndi kutsiriza kwake kudzakhala kwa chigumula, ndi kufikira chimaliziro kudzakhala nkhondo; chipasuko chalembedweratu.