ndi kunena za Kirusi, Iye ndiye mbusa wanga, ndipo adzachita zofuna zanga zonse; ndi kunena za Yerusalemu, Adzamangidwa; ndi kwa Kachisi, Maziko ako adzaikidwa.
Danieli 2:39 - Buku Lopatulika Ndi pambuyo pa inu padzauka ufumu wina wochepa ndi wanu, ndi ufumu wina wachitatu wamkuwa wakuchita ufumu padziko lonse lapansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndi pambuyo pa inu padzauka ufumu wina wochepa ndi wanu, ndi ufumu wina wachitatu wamkuwa wakuchita ufumu pa dziko lonse lapansi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Pambuyo pa inu, ufumu wina udzadzuka, wochepa mphamvu poyerekeza ndi wanuwu. Padzabweranso ufumu wachitatu, wamkuwa, udzalamulira dziko lonse lapansi. |
ndi kunena za Kirusi, Iye ndiye mbusa wanga, ndipo adzachita zofuna zanga zonse; ndi kunena za Yerusalemu, Adzamangidwa; ndi kwa Kachisi, Maziko ako adzaikidwa.
Pamenepo anati, Kodi udziwa chifukwa choti ndakudzera? Ndipo tsopano ndibwerera kulimbana ndi kalonga wa Persiya; ndipo pomuka ine, taonani, adzadza kalonga wa Agriki.
Fano ili tsono, mutu wake unali wagolide wabwino, chifuwa chake ndi manja ake zasiliva, mimba yake ndi chuuno chake zamkuwa,
ndipo paliponse pokhala ana a anthu Iye anapereka nyama zakuthengo, ndi mbalame za m'mlengalenga, m'dzanja lanu; nakuchititsani ufumu pa izi zonse; inu ndinu mutuwo wagolide.
Ndi ufumu wachinai udzakhala wolimba ngati chitsulo, popeza chitsulo chiphwanya ndi kufoketsa zonse; ndipo monga chitsulo chiswa zonsezi, uwu udzaphwanya ndi kuswa.
Anatero, chilombo chachinai ndicho ufumu wachinai padziko lapansi, umene udzasiyana nao maufumu onse, nudzalusira dziko lonse lapansi, nudzalipondereza ndi kuliphwanya.
Ndi tonde wamanyenje ndiye mfumu ya Agriki, ndi nyanga yaikulu ili pakati pamaso ake ndiyo mfumu yoyamba.
Galeta wa akavalo akuda atulukira kudziko la kumpoto; ndi oyerawo atulukira kuwatsata; ndi amawanga atulukira kudziko la kumwera.