Danieli 7:23 - Buku Lopatulika23 Anatero, chilombo chachinai ndicho ufumu wachinai padziko lapansi, umene udzasiyana nao maufumu onse, nudzalusira dziko lonse lapansi, nudzalipondereza ndi kuliphwanya. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201423 Anatero, chilombo chachinai ndicho ufumu wachinai pa dziko lapansi, umene udzasiyana nao maufumu onse, nudzalusira dziko lonse lapansi, nudzalipondereza ndi kuliphwanya. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero23 “Tsono anandifotokozera kuti, ‘Chirombo chachinayi chija ndi ufumu wachinayi umene udzaoneka pa dziko lapansi. Udzakhala wosiyana ndi maufumu anzake onse ndipo udzawononga dziko lonse lapansi. Udzalipondaponda ndi kuliphwasula. Onani mutuwo |
Pambuyo pake ndinaona m'masomphenya a usiku, ndi kuona chilombo chachinai, choopsa ndi chochititsa mantha, ndi champhamvu choposa, chinali nao mano aakulu achitsulo, chinalusa ndi kuphwanya ndi kupondereza chotsala ndi mapazi ake; chinasiyana ndi zilombo zonse zidachitsogolera; ndipo chinali ndi nyanga khumi.