Danieli 7:22 - Buku Lopatulika22 ndi mlandu unakomera opatulika a Wam'mwambamwamba, nifika nthawi yakuti ufumu unali wao wa opatulikawo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201422 ndi mlandu unakomera opatulika a Wam'mwambamwamba, nifika nthawi yakuti ufumu unali wao wa opatulikawo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero22 mpaka pamene Mkulu Wachikhalire uja anafika ndi kuweruza mokomera oyera mtima a Wammwambamwamba. Tsono nthawi inafika imene anthu oyera mtimawo analandira ufumu. Onani mutuwo |
Ndipo ndinaona mipando yachifumu, ndipo anakhala pamenepo; ndipo anawapatsa chiweruziro; ndipo ndinaona mizimu ya iwo amene adawadula khosi chifukwa cha umboni wa Yesu, ndi chifukwa cha mau a Mulungu, ndi iwo amene sanalambire chilombo, kapena fano lake, nisanalandire lembalo pamphumi ndi padzanja lao; ndipo anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Khristu zaka chikwi.