Ndipo anthu onse a padziko anafuna nkhope ya Solomoni, kudzamva nzeru zake zimene Mulungu analonga m'mtima mwake.
Danieli 2:21 - Buku Lopatulika pakuti amasanduliza nthawi ndi nyengo, achotsa mafumu, nalonga mafumu, apatsa anzeru nzeru, ndi chidziwitso kwa iwo okhoza kuzindikira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pakuti amasanduliza nthawi ndi nyengo, achotsa mafumu, nalonga mafumu, apatsa anzeru nzeru, ndi chidziwitso kwa iwo okhoza kuzindikira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amasintha nthawi ndi nyengo; amakweza mafumu ndipo amawatsitsanso. Amapatsa nzeru kwa anzeru ndi chidziwitso kwa ozindikira zinthu. |
Ndipo anthu onse a padziko anafuna nkhope ya Solomoni, kudzamva nzeru zake zimene Mulungu analonga m'mtima mwake.
Ndipo Aisraele onse anamva maweruzidwe ake idaweruza mfumu, naopa mfumu; pokhala anaona kuti nzeru ya Mulungu inali mwa iye yakuweruza.
Ndipo Mulungu anampatsa Solomoni nzeru ndi luntha lambiri, ndi mtima wodziwa za mitundumitundu, zonga mchenga uli m'mphepete mwa nyanja.
Chokhachi, Yehova akupatse nzeru ndi luntha, nakulangize za Israele, kuti usunge chilamulo cha Yehova Mulungu wako.
pamodzi ndi za ufumu wake wonse, ndi mphamvu yake, ndi za nthawizo zidampitira iye, ndi Israele, ndi maufumu onse a maiko.
Pamenepo mfumu inanena kwa eni nzeru, akudziwa za m'tsogolo, mfumu inkatero nao onse akudziwa malamulo ndi maweruzo,
ndipo ndamdzaza ndi mzimu wa Mulungu, ndi luso, ndi nzeru, ndi chidziwitso, ndi m'ntchito zilizonse,
Ndipo Ine, taona, ndampatsa Oholiyabu, mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani, akhale naye; ndipo ndaika luso m'mitima ya onse a mtima waluso, kuti apange zonse ndakuuza iwe;
Koma anyamata amene anai, Mulungu anawapatsa chidziwitso ndi luntha la m'mabuku ali onse, ndi nzeru; koma Daniele anali nalo luntha la m'masomphenya ndi maloto onse.
Chaka chachitatu cha Kirusi mfumu ya Persiya, chinavumbulutsidwa chinthu kwa Daniele, amene anamutcha Belitesazara; ndipo chinthucho nchoona, ndicho nkhondo yaikulu; ndipo anazindikira chinthucho, nadziwa masomphenyawo.
Ndipo pakutha zaka adzaphatikizana iwo; ndi mwana wamkazi wa mfumu ya kumwera adzafika kwa mfumu ya kumpoto, kupangana naye zoyenera; koma mkaziyo sadzaisunga mphamvu ya dzanja lake; ngakhale mwamunayo sadzaimika, ngakhale dzanja lake; koma mkaziyo adzaperekedwa, pamodzi ndi iwo adadza naye, ndi iye amene anambala, ndi iye amene anamlimbitsa nthawi zija.
Daniele anayankha, nati, Lilemekezedwe dzina la Mulungu kunthawi za nthawi, pakuti nzeru ndi mphamvu zili zake;
Ndikuyamikani ndi kukulemekezani Inu, Mulungu wa makolo anga, pakuti mwandipatsa nzeru ndi mphamvu; ndipo mwandidziwitsa tsopano ichi tachifuna kwa Inu; pakuti mwatidziwitsa mlandu wa mfumu.
Koma mukapanda kundidziwitsa lotoli, mlandu wanu ndi umodzi; popeza mwapanganiranatu mau onama ndi oipa, kuwanena pamaso panga, mpaka idzasanduka nyengo; chifukwa chake mundifotokozere lotoli, momwemo ndidzadziwa kuti mudzandidziwitsa kumasulira kwake komwe.
Anafuulitsa, natero, Likhani mtengowo, sadzani nthambi zake, yoyolani masamba ake, mwazani zipatso zake, nyama zakuthengo zichoke pansi pake, ndi mbalame pa nthambi zake.
Chitsutso ichi adachilamulira amithenga oyerawo, anachifunsa, nachinena, kuti amoyo adziwe kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna, nauutsira wolubukira anthu.
ndinu, mfumu; mwakula, mwalimba, pakuti ukulu wanu wakula, nufikira kumwamba, ndi ufumu wanu ku chilekezero cha dziko lapansi.
Nadzakuinga kukuchotsa kwa anthu, ndi pokhala pako udzakhala pamodzi ndi nyama zakuthengo; adzakudyetsa udzu ngati ng'ombe; ndipo zidzakupitira nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka udzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini.
Nidzanena mau akutsutsana ndi Wam'mwambamwamba, nidzalemetsa opatulika a Wam'mwambamwamba, nidzayesa kusintha nthawizo ndi chilamulo; ndipo adzaperekedwa m'dzanja lake mpaka nthawi imodzi, ndi nthawi zina, ndi nthawi yanusu.
Pakuti Ine ndidzakupatsani inu kamwa ndi nzeru, zimene adani anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.
Anthu onse amvere maulamuliro a akulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu; ndipo iwo amene alipo aikidwa ndi Mulungu.
Koma kwa Iye muli inu mwa Khristu Yesu, amene anayesedwa kwa ife nzeru ya kwa Mulungu, ndi chilungamo ndi chiyeretso ndi chiombolo;
Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.
Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.
Ndipo ali nalo pa chovala chake ndi pa ntchafu yake dzina lolembedwa, MFUMU YA MAFUMU, NDI MBUYE WA AMBUYE.