Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 11:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo pakutha zaka adzaphatikizana iwo; ndi mwana wamkazi wa mfumu ya kumwera adzafika kwa mfumu ya kumpoto, kupangana naye zoyenera; koma mkaziyo sadzaisunga mphamvu ya dzanja lake; ngakhale mwamunayo sadzaimika, ngakhale dzanja lake; koma mkaziyo adzaperekedwa, pamodzi ndi iwo adadza naye, ndi iye amene anambala, ndi iye amene anamlimbitsa nthawi zija.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo pakutha zaka adzaphatikizana iwo; ndi mwana wamkazi wa mfumu ya kumwera adzafika kwa mfumu ya kumpoto, kupangana naye zoyenera; koma mkaziyo sadzaisunga mphamvu ya dzanja lake; ngakhale mwamunayo sadzaimika, ngakhale dzanja lake; koma mkaziyo adzaperekedwa, pamodzi ndi iwo adadza naye, ndi iye amene anambala, ndi iye amene anamlimbitsa nthawi zija.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Patapita zaka zingapo, mfumu ya kummwera ndi mfumu ya kumpoto adzachita pangano. Mwana wamkazi wa mfumu ya kummwera adzapita nakakwatiwa ndi mfumu ya kumpoto pokhazikitsa pangano la mtendere, koma ulamuliro wake pamodzi ndi wa mwana wake sudzakhalitsa. Mʼmasiku amenewo iye, mwamuna wake, mwana wake ndi atumiki ake, onse adzaperekedwa kwa adani.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 11:6
9 Mawu Ofanana  

ndi kuunika kwa oipa kuletsedwa kuti asakuone, ndi dzanja losamulidwa lithyoledwa.


Mayendedwe ake alimbika nthawi zonse; maweruzo anu ali pamwamba posaona iye; adani ake onse awanyodola.


Wobadwa ndi munthu iwe, ndathyola dzanja la Farao mfumu ya Aejipito, ndipo taona, silinamangidwe kuti lipole, kulikulunga ndi nsalu, kulilimbitsa ligwire lupanga.


Ndi mfumu ya kumpoto idzabwera, nidzaimika unyinji wakuposa oyamba aja; nidzafika pachimaliziro cha nthawi, cha zaka, ndi khamu lalikulu la nkhondo ndi chuma chambiri.


Ndi mfumu ya kumpoto idzadza, nidzaunda mtumbira, nidzalanda mizinda yamalinga; ndi ankhondo a kumwera sadzalimbika, ngakhale anthu ake osankhika; inde sipadzakhala mphamvu yakulimbika.


Ndipo nthawi yotsiriza mfumu ya kumwera idzalimbana naye, ndi mfumu ya kumpoto idzamdzera ngati kamvulumvulu, ndi magaleta, ndi apakavalo, ndi zombo zambiri; nadzalowa m'maiko, nadzasefukira ndi kupitirira.


Koma apo pophukira mizu yake adzauka wina m'malo mwake, ndiye adzafika kulimbana nalo khamu la nkhondo, nadzalowa m'linga la mfumu ya kumpoto, nadzachita molimbana nao, nadzawagonjetsa;


Pakuti taonani, ndidzautsa mbusa m'dziko amene sadzazonda otayika, kapena kufunafuna zomwazika, kapena kulunzitsa yothyoka, kapena kudyetsa yamoyo, koma adzadya nyama ya zonenepa, nadzang'amba ziboda zao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa