Danieli 11:7 - Buku Lopatulika7 Koma apo pophukira mizu yake adzauka wina m'malo mwake, ndiye adzafika kulimbana nalo khamu la nkhondo, nadzalowa m'linga la mfumu ya kumpoto, nadzachita molimbana nao, nadzawagonjetsa; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Koma apo pophukira mizu yake adzauka wina m'malo mwake, ndiye adzafika kulimbana nalo khamu la nkhondo, nadzalowa m'linga la mfumu ya kumpoto, nadzachita molimbana nao, nadzawalaka; Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 “Mmodzi wochokera ku banja la mkaziyo adzadzuka nadzalamulira mʼmalo mwake. Iye adzamenyana ndi ankhondo a mfumu ya kumpoto ndi kulowa mʼmalo ake otetezedwa; adzachita nawo nkhondo ndi kupambana. Onani mutuwo |
Ndipo pakutha zaka adzaphatikizana iwo; ndi mwana wamkazi wa mfumu ya kumwera adzafika kwa mfumu ya kumpoto, kupangana naye zoyenera; koma mkaziyo sadzaisunga mphamvu ya dzanja lake; ngakhale mwamunayo sadzaimika, ngakhale dzanja lake; koma mkaziyo adzaperekedwa, pamodzi ndi iwo adadza naye, ndi iye amene anambala, ndi iye amene anamlimbitsa nthawi zija.