Danieli 11:7 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 “Mmodzi wochokera ku banja la mkaziyo adzadzuka nadzalamulira mʼmalo mwake. Iye adzamenyana ndi ankhondo a mfumu ya kumpoto ndi kulowa mʼmalo ake otetezedwa; adzachita nawo nkhondo ndi kupambana. Onani mutuwoBuku Lopatulika7 Koma apo pophukira mizu yake adzauka wina m'malo mwake, ndiye adzafika kulimbana nalo khamu la nkhondo, nadzalowa m'linga la mfumu ya kumpoto, nadzachita molimbana nao, nadzawagonjetsa; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Koma apo pophukira mizu yake adzauka wina m'malo mwake, ndiye adzafika kulimbana nalo khamu la nkhondo, nadzalowa m'linga la mfumu ya kumpoto, nadzachita molimbana nao, nadzawalaka; Onani mutuwo |
Patapita zaka zingapo, mfumu ya kummwera ndi mfumu ya kumpoto adzachita pangano. Mwana wamkazi wa mfumu ya kummwera adzapita nakakwatiwa ndi mfumu ya kumpoto pokhazikitsa pangano la mtendere, koma ulamuliro wake pamodzi ndi wa mwana wake sudzakhalitsa. Mʼmasiku amenewo iye, mwamuna wake, mwana wake ndi atumiki ake, onse adzaperekedwa kwa adani.