Chifukwa inu munati, Ife tapangana pangano ndi imfa, tavomerezana ndi kunsi kwa manda; pakuti mliri wosefukira sudzatifikira ife; pakuti tayesa mabodza pothawirapo pathu, ndi kubisala m'zonyenga;
Danieli 11:22 - Buku Lopatulika Ndipo mwa mayendedwe ake a chigumula adzakokololedwa pamaso pake, nadzathyoledwa, ngakhale kalonga yemwe wa chipangano. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mwa mayendedwe ake a chigumula adzakokololedwa pamaso pake, nadzathyoledwa, ngakhale kalonga yemwe wa chipangano. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka adzagonetsa gulu lalikulu lankhondo kuphatikizapo Mkulu wa Ansembe wapangano. |
Chifukwa inu munati, Ife tapangana pangano ndi imfa, tavomerezana ndi kunsi kwa manda; pakuti mliri wosefukira sudzatifikira ife; pakuti tayesa mabodza pothawirapo pathu, ndi kubisala m'zonyenga;
Ndi ana ake adzachita nkhondo, nadzamemeza makamu a nkhondo aakulu ochuluka, amene adzalowa, nadzasefukira, nadzapita; ndipo adzabwerera, nadzachita nkhondo mpaka linga lake.
Ndipo atapangana naye adzachita monyenga; pakuti adzakwera, nadzasanduka wamphamvu ndi anthu owerengeka.
Ndipo mwa kuchenjera kwake adzapindulitsa chinyengo m'dzanja mwake, nadzadzikuza m'mtima mwake; ndipo posatekeseka anthu, adzaononga ambiri; adzaukiranso kalonga wa akalonga, koma adzathyoledwa popanda dzanja.
Ndipo atapita masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri wodzozedwayo adzalikhidwa, nadzakhala wopanda kanthu; ndi anthu a kalonga wakudzayo adzaononga mzinda ndi malo opatulika; ndi kutsiriza kwake kudzakhala kwa chigumula, ndi kufikira chimaliziro kudzakhala nkhondo; chipasuko chalembedweratu.
Kodi dziko silidzanjenjemera chifukwa cha ichi, ndi kulira aliyense wokhalamo? Inde lidzakwera lonseli ngati madzi a m'mtsinje; lidzagwezeka, ndi kutsikanso ngati mtsinje wa Ejipito.
Pakuti Ambuye Yehova wa makamu ndiye amene akhudza dziko, nilisungunuka; ndi onse okhalamo adzachita maliro; ndipo lidzakwera lonseli ngati madzi a m'mtsinje; nilidzatsikanso ngati mtsinje wa mu Ejipito;
Koma ndi chigumula chosefukira adzatha konse malo ake, nadzapirikitsira adani ake kumdima.