Danieli 11:10 - Buku Lopatulika10 Ndi ana ake adzachita nkhondo, nadzamemeza makamu a nkhondo aakulu ochuluka, amene adzalowa, nadzasefukira, nadzapita; ndipo adzabwerera, nadzachita nkhondo mpaka linga lake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Ndi ana ake adzachita nkhondo, nadzamemeza makamu a nkhondo akulu ochuluka, amene adzalowa, nadzasefukira, nadzapita; ndipo adzabwerera, nadzachita nkhondo mpaka linga lake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Ana ake adzakonzekera nkhondo ndi kusonkhanitsa gulu lankhondo lalikulu, limene lidzathira nkhondo mfumu yakummwera ngati chigumula mpaka kumalo ake otetezedwa. Onani mutuwo |
Ndipo atapita masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri wodzozedwayo adzalikhidwa, nadzakhala wopanda kanthu; ndi anthu a kalonga wakudzayo adzaononga mzinda ndi malo opatulika; ndi kutsiriza kwake kudzakhala kwa chigumula, ndi kufikira chimaliziro kudzakhala nkhondo; chipasuko chalembedweratu.