Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 9:5 - Buku Lopatulika

5 Pakuti Ambuye Yehova wa makamu ndiye amene akhudza dziko, nilisungunuka; ndi onse okhalamo adzachita maliro; ndipo lidzakwera lonseli ngati madzi a m'mtsinje; nilidzatsikanso ngati mtsinje wa mu Ejipito;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Pakuti Ambuye Yehova wa makamu ndiye amene akhudza dziko, nilisungunuka; ndi onse okhalamo adzachita maliro; ndipo lidzakwera lonseli ngati madzi a m'nyanja; nilidzatsikanso ngati nyanja ya m'Ejipito;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Ambuye Chauta Wamphamvuzonse, akakhudza dziko, limanyenyeka, ndipo zonse zokhala m'menemo zimalira. Apo dziko lonse limafufuma ngati mtsinje wa Nailo ndipo limateranso ngati mtsinje wa Nailo wa ku Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Ambuye Yehova Wamphamvuzonse amene amakhudza dziko lapansi ndipo dzikolo limasungunuka, onse amene amakhala mʼmenemo amalira. Dziko lonse lidzadzaza ngati mtsinje wa Nailo, kenaka nʼkuphwera ngati mtsinje wa ku Igupto.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 9:5
17 Mawu Ofanana  

amene apenyerera padziko lapansi, ndipo linjenjemera; akhudza mapiri, ndipo afuka.


Weramutsani thambo lanu, Yehova, nimutsike: Khudzani mapiri ndipo adzafuka.


Chifukwa chake oyera mtima onse apemphere kwa Inu, pa nthawi ya kupeza Inu; indetu pakusefuka madzi aakulu sadzamfikira iye.


Amitundu anapokosera, maufumu anagwedezeka, ananena mau, dziko lapansi linasungunuka.


Mapiri anasungunuka ngati sera pamaso pa Yehova, pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi.


Mwenzi mutang'amba kumwamba ndi kutsikira pansi, kuti mapiri agwedezeke pamaso panu;


Dziko lidzalira masiku angati, nilifota therere la minda yonse? Chifukwa cha zoipa za iwo okhalamo, zithedwa zinyama, ndi mbalame; pakuti iwo anati, Iye sadzaona chitsiriziro chathu.


Chifukwa chake dziko lidzachita chisoni, ndi aliyense wokhalamo adzalefuka, pamodzi ndi nyama zakuthengo, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndi nsomba za m'nyanja zomwe zidzachotsedwa.


Kodi dziko silidzanjenjemera chifukwa cha ichi, ndi kulira aliyense wokhalamo? Inde lidzakwera lonseli ngati madzi a m'mtsinje; lidzagwezeka, ndi kutsikanso ngati mtsinje wa Ejipito.


Mapiri agwedezeka chifukwa cha Iye, ndi zitunda zisungunuka; ndi dziko lapansi likwezeka pamaso pake, ndi maiko ndi onse okhala m'mwemo.


Adzaima ndani pa kulunda kwake? Ndipo adzakhalitsa ndani pa mkwiyo wake wotentha? Ukali wake utsanulidwa ngati moto, ndi matanthwe asweka ndi Iye.


Mapiri anakuonani, namva zowawa; chigumula cha madzi chinapita; madzi akuya anamveketsa mau ake, nakweza manja ake m'mwamba.


ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; ndipo inagwa; ndi kugwa kwake kunali kwakukulu.


Ndipo ndinaona, mpando wachifumu waukulu woyera, ndi Iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pake, ndipo sanapezedwe malo ao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa