Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 9:6 - Buku Lopatulika

6 ndiye amene amanga zipinda zake zosanja m'mwamba, nakhazika tsindwi lake padziko lapansi; Iye amene aitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira padziko; dzina lake ndiye Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 ndiye amene amanga zipinda zake zosanja m'mwamba, nakhazika tsindwi lake pa dziko lapansi; Iye amene aitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira padziko; dzina lake ndiye Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Ndiwo amene amamanga malo ao okhalamo kumwamba, naika thambo ngati denga la dziko lapansi, amaitana madzi akunyanja naŵakhuthulira pa dziko lapansi. Iwowo dzina lao ndi Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Iye amene amamanga malo ake okhalamo kumwamba, ndi kuyika maziko ake pa dziko lapansi, Iye amene amayitana madzi a ku nyanja ndikuwakhuthulira pa dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 9:6
9 Mawu Ofanana  

Ndipo zinatha kupangidwa zakumwamba ndi dziko lapansi, ndi khamu lao lonse.


Iye amwetsa mapiri mochokera m'zipinda zake: Dziko lakhuta zipatso za ntchito zanu.


Amene alumikiza mitanda ya zipinda zake m'madzi; naika makongwa akhale agaleta ake; nayenda pa mapiko a mphepo.


Kodi simundiopa Ine? Ati Yehova: simudzanthunthumira pamaso pa Ine, amene ndinaika mchenga chilekaniro cha nyanja, ndi lemba lamuyaya kuti isapitirirepo? Ndipo ngakhale mafunde ake achita gavigavi, alephera; ngakhale akokoma, sangathe kupitirirapo.


Pakuti taona, Iye amene aumba mapiri, nalenga mphepo, nafotokozera munthu maganizo ake, nasanduliza m'mawa ukhale mdima, naponda pa misanje ya dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova Mulungu wa makamu.


Iye wakulenga Nsangwe ndi Akamwiniatsatana, nasanduliza mdima wandiweyani ukhale m'mawa, nasanduliza usana ude ngati usiku, wakuitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira padziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa