Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 9:7 - Buku Lopatulika

7 Kodi simukhala kwa Ine ngati ana a Kusi, inu ana a Israele? Ati Yehova. Sindinakweza Israele ndine, kumtulutsa m'dziko la Ejipito, ndi Afilisti ku Kafitori, ndi Aaramu ku Kiri?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Kodi simukhala kwa Ine ngati ana a Kusi, inu ana a Israele? Ati Yehova. Sindinakweza Israele ndine, kumtulutsa m'dziko la Ejipito, ndi Afilisti ku Kafitori, ndi Aaramu ku Kiri?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 “Kwa Ine, Aisraelenu muli ngati Aetiopiya.” Akuterotu Chauta. “Kodi sindine uja ndidatulutsa Aisraele ku Ejipito? Kodi sindine uja ndidatulutsa Afilisti ku Kafitori ndi Asiriya ku Kiri?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 “Kodi kwa Ine, inu Aisraeli, simuli chimodzimodzi ndi Akusi?” Akutero Yehova. “Kodi sindine amene ndinatulutsa Israeli ku Igupto, Afilisti ku Kafitori ndi Aaramu ku Kiri?

Onani mutuwo Koperani




Amosi 9:7
14 Mawu Ofanana  

Nimmvera mfumu ya Asiriya, nikwera kunka ku Damasiko mfumu ya Asiriya, niulanda, nipita nao anthu ake andende ku Kiri, nimupha Rezini.


Ndipo Yehova anakantha Akusi pamaso pa Asa ndi Yuda, nathawa Akusi.


Ndipo anawatulukira Zera Mkusi ndi ankhondo zikwi chikwi chimodzi, ndi magaleta mazana atatu; nafika iye ku Maresa.


Ndipo kunakhala tsiku lomwelo, kuti Yehova anatulutsa ana a Israele m'dziko la Ejipito, monga mwa makamu ao.


momwemo mfumu ya Asiriya idzatsogolera kwina am'nsinga a Ejipito, ndi opirikitsidwa a Etiopiya, ana ndi okalamba, amaliseche ndi opanda nsapato, ndi matako osavala, kuti achititse manyazi Ejipito.


Ndipo Elamu anatenga phodo, ndi magaleta a anthu ndi apakavalo; ndipo Kiri anaonetsa zikopa.


Chifukwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wako, Woyera wa Israele, Mpulumutsi wako; ndapatsa Ejipito dombolo lako, Etiopiya ndi Seba m'malo mwako.


Kodi angathe Mkusi kusanduliza khungu lake, kapena nyalugwe mawanga ake? Pamenepo mungathe inunso kuchita zabwino, inu amene muzolowera kuchita zoipa.


chifukwa cha tsiku lakudzafunkha Afilisti onse, kuphera Tiro ndi Sidoni othangata onse akutsala; pakuti Yehova adzafunkha Afilisti, otsala a chisumbu cha Kafitori.


Ndipo mwa mneneri Yehova anakweretsa Israele kuchokera mu Ejipito, ndi mwa mneneri anasungika.


Ndipo ndidzathyola mpiringidzo wa Damasiko, ndi kulikha okhala m'chigwa cha Aveni, ndi iye wogwira ndodo yachifumu mu Betedeni; ndi anthu a Aramu adzalowa ndende ku Kiri, ati Yehova.


Ndipo ndinakukwezani kuchokera m'dziko la Ejipito, ndi kukutsogolerani zaka makumi anai m'chipululu, kuti mulandire dziko la Aamori likhale cholowa chanu.


Kunena za Aavimu akukhala m'midzi kufikira ku Gaza, Akafitori, akufuma ku Kafitori, anawaononga, nakhala m'malo mwao).


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa