Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 9:4 - Buku Lopatulika

4 Angakhale alowa ndende pamaso pa adani ao, kumeneko ndidzalamulira lupanga, ndipo lidzawapha; ndipo ndidzayang'anitsa maso anga kwa iwowa, kuwachitira choipa, si chokoma ai.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Angakhale alowa ndende pamaso pa adani ao, kumeneko ndidzalamulira lupanga, ndipo lidzawapha; ndipo ndidzayang'anitsa maso anga kwa iwowa, kuwachitira choipa, si chokoma ai.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ngakhale adani ao aŵakusire ku ukapolo, komweko ndidzalamula kuti aphedwe pa nkhondo. Ndidzaŵayang'anitsitsa kuti ziŵagwere zoipa osati zabwino.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Ngakhale adani awo awakusire ku ukapolo, ndidzalamula lupanga kuti liwaphe kumeneko. Ndidzawayangʼanitsitsa kuti zoyipa ziwagwere; osati zabwino.”

Onani mutuwo Koperani




Amosi 9:4
20 Mawu Ofanana  

Ndipo munati kwa akapolo anu, Munditengere iye, kuti ndimuone iye m'maso mwanga.


Pakuti maso a Yehova ayang'ana uko ndi uko m'dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wao uli wangwiro ndi Iye. Mwachita chopusa m'menemo; pakuti kuyambira tsopano mudzaona nkhondo.


Iwowo anaitana, ndipo Yehova anawamva, nawalanditsa kumasautso ao onse.


Ndipo kunali, ulonda wa mamawa, Yehova ali m'moto ndi m'mtambo njo anapenyera pa ulendo wa Aejipito, nauvuta ulendo wa Aejipito.


Akufunkha afika pa mapiri oti see m'chipululu; pakuti lupanga la Yehova lilusa kuyambira pa mbali ina ya dziko kufikira kumbali ina; palibe thupi lokhala ndi mtendere.


Pakuti ndaika nkhope yanga pa mzinda uwu ndiuchitire choipa, si chabwino, ati Yehova; ndipo udzapatsidwa m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzautentha ndi moto.


Pakuti ndidzaika maso anga pa iwo kuti ndiwachitire iwo bwino, ndipo ndidzawabwezanso kudziko ili: ndipo ndidzamangitsa mudzi wao, osawapasula; ndi kuwabzala, osawazula iwo.


Umtenge, numyang'anire bwino, usamsautse, koma umchitire monga iye adzanena nawe.


Pita, ukanene kwa Ebedemeleki Mkusi, kuti, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taona, ndidzafikitsira mzinda uwu mau anga kuusautsa, osauchitira zabwino; ndipo adzachitidwa pamaso pako tsiku lomwelo.


Chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani, ndidzayang'anitsa nkhope yanga pa inu ndikuchitireni inu choipa, ndidule Yuda yense.


Limodzi la magawo atatu la iwe lidzafa ndi mliri, nilidzatha ndi njala pakati pa iwe; ndi limodzi lidzagwa ndi lupanga pozinga pako; ndi limodzi ndidzalibalalikitsa kumphepo zonse, ndi kuwasololera lupanga lakuwatsata.


Limodzi la magawo ake atatu utenthe ndi moto pakati pa mzinda pakutha masiku a kuzingidwa mzinda, nutenge gawo lina ndi kukwapulakwapula ndi lupanga pozungulira pake, nuwaze kumphepo gawo lotsala; pakuti ndidzasolola lupanga lakuwatsata.


Ndipo munthu aliyense wa mbumba ya Israele, kapena mlendo wogonera pakati panu, wakudya mwazi uliwonse; nkhope yanga idzatsutsana naye munthu wakudya mwaziyo, ndi kumsadza kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.


Ndipo ndidzabalalitsa inu mwa amitundu, ndi kusolola lupanga kukutsatani; ndi dziko lanu lidzakhala lopasuka, ndi mizinda yanu idzakhala bwinja.


Taonani, maso a Ambuye Yehova ali pa ufumu wochimwawo, ndipo ndidzauononga kuuchotsa padziko lapansi; pokhapo sindidzaononga nyumba ya Yakobo kuitha konse, ati Yehova.


Pakuti asanafike masiku aja, panalibe kulipidwira munthu, kapena kulipidwira nyama, ndipo analibe mtendere iye wakutuluka, kapena wakulowa, chifukwa cha wosautsa; pakuti ndinatumiza munthu yense atsutsane naye mnzake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa