Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 9:3 - Buku Lopatulika

3 Angakhale abisala pamwamba pa Karimele, ndidzawapwaira ndi kuwatenga komweko; angakhale abisala pamaso panga pansi pa nyanja, kumeneko ndidzalamulira njoka, ndipo idzawaluma.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Angakhale abisala pamwamba pa Karimele, ndidzawapwaira ndi kuwatenga komweko; angakhale abisala pamaso panga pansi pa nyanja, kumeneko ndidzalamulira njoka, ndipo idzawaluma.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Ngakhale akabisale pamwamba pa phiri la Karimele, ndidzaŵaunguza nkuŵagwira. Ngakhale akabisale pansi pa nyanja yaikulu, ndidzalamula chilombo cham'nyanjamo kuti chiŵalume.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Ngakhale atakabisala pamwamba pa phiri la Karimeli, Ine ndidzawasaka kumeneko ndi kuwagwira. Ngakhale atakabisala pansi pa nyanja yayikulu, ndidzalamula njoka kuti iwalume kumeneko.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 9:3
10 Mawu Ofanana  

Ndipo anamva mau a Yehova Mulungu alinkuyendayenda m'munda nthawi yamadzulo: ndipo anabisala Adamu ndi mkazi wake pamaso pa Yehova Mulungu pakati pamitengo ya m'munda.


Alendo adzafota, nadzabwera ndi kunthunthumira otuluka mokwiririka mwao.


Ndipo ukuti, Adziwa chiyani Mulungu? Aweruza kodi mwa mdima wa bii?


Palibe mdima kapena mthunzi wa imfa, kuti ochita zopanda pake abisaleko.


kuti uviike phazi lako m'mwazi, kuti malilime a agalu ako alaweko adani ako.


Tsiku limenelo Yehova ndi lupanga lake lolimba ndi lalikulu ndi lamphamvu adzalanga Leviyatani njoka yothamanga, ndi Leviyatani njoka yopindikapindika; nadzapha ching'ona chimene chili m'nyanja.


Taonani, ndidzaitana akugwira nsomba ambiri, ati Yehova, ndipo adzawagwira iwo, pambuyo pake ndidzaitana osaka nyama ambiri, ndipo adzasaka iwo m'mapiri onse, ndi pa zitunda zonse, ndiponso m'mapanga a m'matanthwe.


Ndipo anati, Yehova adzadzuma ali mu Ziyoni, nadzamveketsa mau ake ali mu Yerusalemu; podyetsa abusa padzachita chisoni, ndi mutu wa Karimele udzauma.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa