Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 9:2 - Buku Lopatulika

2 Angakhale akumba mpaka kunsi kwa manda, dzanja langa lidzawatenga kumeneko; angakhale akwera kumwamba, ndidzawatsitsa komweko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Angakhale akumba mpaka kunsi kwa manda, dzanja langa lidzawatenga kumeneko; angakhale akwera kumwamba, ndidzawatsitsa komweko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 “Ngakhale akakumbe pansi mpaka ku malo a anthu akufa, dzanja langa lidzaŵadukhululako kumeneko. Ngakhale akakwere mpaka kumwamba, ndidzaŵatsakamutsako.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ngakhale atakumba pansi mpaka ku malo a anthu akufa, dzanja langa lidzawatulutsa kumeneko. Ngakhale atakwera kumwamba Ine ndidzawatsakamutsa kumeneko.

Onani mutuwo Koperani




Amosi 9:2
15 Mawu Ofanana  

Chinkana ukulu wake ukwera kunka kuthambo, nugunda pamitambo mutu wake;


Ndipo ukuti, Adziwa chiyani Mulungu? Aweruza kodi mwa mdima wa bii?


Awalola akhale osatekeseka, ndipo alimbikapo; koma maso ake ali panjira zao.


Kumanda kuli padagu pamaso pake, ndi kuchionongeko kusowa chophimbako.


Palibe mdima kapena mthunzi wa imfa, kuti ochita zopanda pake abisaleko.


Anthu adzalowa m'mapanga a m'matanthwe, ndi m'maenje apansi, kuthawa kuopsa kwa Yehova, ndi ulemerero wachifumu wake, podzuka Iye kugwedeza dziko ndi mphamvu.


Koma za kuopsa kwako, kunyada kwa mtima wako kunakunyenga iwe, wokhala m'mapanga a thanthwe, woumirira msanje wa chitunda, ngakhale usanja chisanja chako pamwamba penipeni ngati chiombankhanga, ndidzakutsitsa iwe kumeneko, ati Yehova.


Ngakhale Babiloni adzakwera kumwamba, ngakhale adzalimbitsa msanje wa mphamvu yake, koma kuchokera kwa Ine akufunkha adzafika kwa iye, ati Yehova.


pamenepo ndidzakutsitsa nao otsikira kumanda, kwa anthu a kale lomwe, ndi kukukhalitsa kumalo a kunsi kwa dziko, kopasukira kale lomwe, pamodzi nao otsikira kumanda, kuti mwa iwe musakhale anthu; ndipo ndidzaika ulemerero m'dziko la amoyo,


kuti mitengo iliyonse ya kumadzi isadzikuze chifukwa cha msinkhu wao, kapena kufikitsa nsonga zao pakati pa mitambo, ndi kuti amphamvu ao asaime m'kukula kwao, ndiwo onse akumwa madzi; pakuti onsewo aperekedwa kuimfa munsi mwake mwa dziko, pakati pa ana a anthu, pamodzi ndi iwo otsikira kumanda.


Chinkana ukwera pamwamba penipeni ngati chiombankhanga, chinkana chisanja chako chisanjika pakati pa nyenyezi, ndidzakutsitsa kumeneko, ati Yehova.


Ndipo anati kwa iwo, Ndinaona Satana alinkugwa ngati mphezi wochokera kumwamba.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa