Amosi 9:1 - Buku Lopatulika1 Ndinaona Ambuye alikuima paguwa la nsembe, nati Iye, Kantha mitu ya nsanamira, kuti ziundo zigwedezeke; nuphwanye mitu yao yonse; ndipo ndidzapha otsiriza ao ndi lupanga; wothawayo mwa iwo sadzathawadi, ndi wopulumukayo mwa iwo sadzapulumukadi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndinaona Ambuye alikuima pa guwa la nsembe, nati Iye, Kantha mitu ya nsanamira, kuti ziundo zigwedezeke; nuphwanye mitu yao yonse; ndipo ndidzapha otsiriza ao ndi lupanga; wothawayo mwa iwo sadzathawadi, ndi wopulumukayo mwa iwo sadzapulumukadi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Tsono ndidaona Chauta ataima pambali pa guwa. Adati, “Gwetsani makapotolosi a Nyumba ya Mulungu, kuti maziko ake agwedezeke. Muŵagwetsere pamitu pa anthu. Onse otsalira Ine ndidzaŵapha pa nkhondo. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathaŵe. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzapulumukepo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Ine ndinaona Ambuye atayima pambali pa guwa lansembe, ndipo anati: “Kantha mitu ya nsanamira kuti ziwundo za nyumba zigwedezeke. Muzigwetsere pa mitu ya anthu onse, onse amene atsalira ndidzawapha ndi lupanga. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathawe, palibe amene adzapulumuke. Onani mutuwo |