Momwemo inalekeka ntchito ya nyumba ya Mulungu yokhala ku Yerusalemu; nilekeka mpaka chaka chachiwiri cha ufumu wa Dariusi mfumu ya Persiya.
Danieli 11:2 - Buku Lopatulika Ndipo tsopano ndikufotokozera choonadi. Taona, adzaukanso mafumu atatu mu Persiya, ndi yachinai idzakhala yolemera ndithu yoposa onsewo; ndipo itadzilimbitsa yokha mwa kulemera kwake idzawautsa onse alimbane nao ufumu wa Agriki. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo tsopano ndikufotokozera choonadi. Taona, adzaukanso mafumu atatu m'Persiya, ndi yachinai idzakhala yolemera ndithu yoposa onsewo; ndipo itadzilimbitsa yokha mwa kulemera kwake idzawautsa onse alimbane nao ufumu wa Agriki. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ndipo tsopano ndikuwuza zoona: Mafumu ena atatu adzalamulira ku Peresiya, ndipo kenaka padzadzuka mfumu yachinayi imene idzakhala yolemera kwambiri kuposa onsewo. Popeza kuti idzakhala ndi mphamvu chifukwa cha chuma chake, idzadzutsa onse kuti alimbane ndi ufumu wa Grisi. |
Momwemo inalekeka ntchito ya nyumba ya Mulungu yokhala ku Yerusalemu; nilekeka mpaka chaka chachiwiri cha ufumu wa Dariusi mfumu ya Persiya.
Ndipo masiku a Arita-kisereksesi Bisilamu, Mitiredati, Tabeele, ndi anzao otsala, analembera kwa Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya; ndi chilembedwe chake cha kalatayo anamlemba mu Chiaramu, namsanduliza mu Chiaramu.
Izi zinachitika masiku a Ahasuwero, ndiye Ahasuweroyo anachita ufumu kuyambira Indiya kufikira Kusi, pa maiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri.
kuti ukadziwitse ntheradi yake ya mau oona, nukabwere ndi mau oona kwa iwo amene anakutumiza?
Chaka chachitatu cha Kirusi mfumu ya Persiya, chinavumbulutsidwa chinthu kwa Daniele, amene anamutcha Belitesazara; ndipo chinthucho nchoona, ndicho nkhondo yaikulu; ndipo anazindikira chinthucho, nadziwa masomphenyawo.
Nadzautsa mphamvu yake ndi mtima wake ayambane ndi mfumu ya kumwera ndi khamu lalikulu la nkhondo; ndi mfumu ya kumwera idzachita nkhondo ndi khamu lalikulu ndi lamphamvu ndithu; koma sadzaimika, popeza adzamlingiririra ziwembu.
Ndipo taonani, chilombo china chachiwiri chikunga chimbalangondo chinatundumuka mbali imodzi; ndi m'kamwa mwake munali nthiti zitatu pakati pa mano ake; ndipo anatero nacho, Nyamuka, lusira nyama zambiri.
Ndi tonde wamanyenje ndiye mfumu ya Agriki, ndi nyanga yaikulu ili pakati pamaso ake ndiyo mfumu yoyamba.
Ndipo masomphenya a madzulo ndi mamawa adanenawo ndi oona; koma iwe ubise masomphenyawo, popeza adzachitika atapita masiku ambiri.
Ndinaona nkhosa yamphongo ilikugunda kumadzulo, ndi kumpoto, ndi kumwera; ndipo panalibe zamoyo zokhoza kuima pamaso pake; panalibenso wakulanditsa m'dzanja lake; koma inachita monga mwa chifuniro chake, nidzikulitsa.
Pakuti Ambuye Yehova sadzachita kanthu osawulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.
Ngati anawatcha milungu iwo amene mau a Mulungu anawadzera (ndipo cholemba sichingathe kuthyoka),
Ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu anati, Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano. Ndipo ananena, Talemba; pakuti mau awa ali okhulupirika ndi oona.